NYIMBO 115

Tiziyamikira Kuleza Mtima kwa Mulungu

Tiziyamikira Kuleza Mtima kwa Mulungu

(2 Petulo 3:15)

  1. 1. Yehova wamphamvu zosatha,

    Mumakondatu zabwino.

    Zoipa n’zambiri m’dziko,

    Mumadziwa n’zosautsa.

    Simukuchedwa tikudziwa;

    Posachedwa mudzazichotsa.

    (KOLASI)

    Tiyembekeza mwachidwi,

    Timatamanda dzina lanu.

  2. 2. Zaka chikwi zilitu ngati,

    Tsiku limodzi kwa inu.

    Tsiku lanu lalikulu;

    Layandikira kwambiri.

    Anthu ochimwa akalapa,

    Mumasangalala kwambiri.

    (KOLASI)

    Tiyembekeza mwachidwi,

    Timatamanda dzina lanu.