NYIMBO 122

Khalani Olimba Komanso Osasunthika

Khalani Olimba Komanso Osasunthika

(1 Akorinto 15:58)

  1. 1. Anthu akuvutika kwambiri

    Ndipo akuopa zam’tsogolo.

    Ife tilimbe tisasunthike

    Potumikira M’lungu.

    (KOLASI)

    Tiyenera kulimba.

    Tisiyane ndi dziko.

    Tikhale olimba.

    Tidzapeza moyo.

  2. 2. Misampha ndi yambiri m’dzikoli

    Koma tingaipewe mwanzeru.

    Tikamadanatu ndi zoipa

    Sitidzasunthikadi.

    (KOLASI)

    Tiyenera kulimba.

    Tisiyane ndi dziko.

    Tikhale olimba.

    Tidzapeza moyo.

  3. 3. Tizilambira Yehova yekha.

    Tim’tumikire ndi mtima wonse.

    Tizilalikiradi mwakhama.

    Mapeto akubwera.

    (KOLASI)

    Tiyenera kulimba.

    Tisiyane ndi dziko.

    Tikhale olimba.

    Tidzapeza moyo.