NYIMBO 130

Muzikhululuka

Muzikhululuka

(Salimo 86:5)

  1. 1. Mwachikondi M’lungu

    Anapereka Yesu

    Kuti tikhululukidwe,

    Ndi kuthetsanso imfa.

    M’lungu amakhululuka,

    Ngati ife talapa.

    Nsembe ya dipo ya Yesu,

    Imatithandizadi.

  2. 2. Tikamatsanzira

    Chifundo cha Yehova

    Pokhululukira ena,

    Tidzakhululukidwa.

    Tikhale ololerana,

    Ndipo tisamadane;

    Tizilemekeza ena,

    Komanso kuwakonda.

  3. 3. Chifundo n’chabwino

    Tonse tikhale nacho.

    Sitidzasunga zifukwa,

    Tikakhumudwitsidwa.

    Tikatsanzira Yehova,

    Yemwe ndi wachikondi,

    Tidzakhululukirana;

    Tidzafanana naye.