NYIMBO 137

Akazi Achikhristu Okhulupirika

Akazi Achikhristu Okhulupirika

(Aroma 16:2)

  1. 1. Sara, Esitere, Rute, ndi ena​—

    Onsewa ’nali akazi abwino,

    Anali odzipereka kwa M’lungu.

    Timawadziwa ndi mayina awo.

    Panali ena sanatchulidwe,

    Iwotu Yehova ankawakondanso.

  2. 2. Akaziwatu amatikumbutsa

    Makhalidwe omwe tifunikira.

    Monga ubwino ndi kulimba mtima.

    Ndi zitsanzo zotilimbikitsadi.

    Alongo a masiku anonso,

    Khalani zitsanzo kwa ena tonsefe.

  3. 3. Achemwali, amayi, amasiye

    Mumachita khama pogwira ntchito

    Mumagonjera, mumadzichepetsa.

    Musaope Mulungu ali nanu.

    Ndipo iye akulimbitseni,

    Musafooketu, mudzadalitsidwa.