NYIMBO 151

Iye Adzaitana

Iye Adzaitana

(Yobu 14:13-15)

  1. 1. Moyo wathu sumachedwa kutha,

    Timafadi mwamsanga.

    Mukanthawi kochepa kwambiri,

    Timayamba kulira.

    Kodi akufa angadzukenso?

    M’lungu akulonjeza:

    (KOLASI)

    Iye adzawaitana;

    Akufa adzayankha.

    Ntchito ya manja ake.

    Adzailakalaka.

    Inu musakayikire,

    M’lungu adzatidzutsa.

    Tidzakhala kosatha,

    Mongadi anthu ake.

  2. 2. Anthu a M’lungu akamwalira,

    Iye sawaiwala.

    Omwe amawakumbukiratu,

    Iye adzawadzutsa.

    Ndipo tonse tidzasangalala

    Ndi moyo m’paradaiso.

    (KOLASI)

    Iye adzawaitana;

    Akufa adzayankha.

    Ntchito ya manja ake.

    Adzailakalaka.

    Inu musakayikire,

    M’lungu adzatidzutsa.

    Tidzakhala kosatha,

    Mongadi anthu ake.