NYIMBO 17

“Ndikufuna”

“Ndikufuna”

(Luka 5:13)

  1. 1. Khristu anasonyezatu,

    Chikondi, kukoma mtima.

    Pobwera padziko,

    n’kutithandiza

    M’mawu komanso zochita;

    Ankakonda ovutika

    Anachiritsa odwala.

    Ndi kukwaniritsa ntchito yake

    Ananena: “Ndikufuna.”

  2. 2. Tifuna kumutsanzira

    M’zonse zomwe timachita.

    Timasonyezatu

    kukoma mtima,

    Pophunzitsa ’nthu kumvera.

    Anzathu akavutika;

    Tiwasonyeze chikondi.

    Choncho amasiye akapempha.

    Tidzanena: “Ndikufuna.”