NYIMBO 25

Chuma Chapadera

Chuma Chapadera

(1 Petulo 2:9)

  1. 1. Odzozedwa ndi mtundu,

    Watsopano wa M’lungu.

    Iye anawagula,

    Padziko lapansi.

    (KOLASI)

    N’chuma chapadera,

    Otchedwa dzina lanu

    Amakukondani.

    Amalengezadi za inu.

  2. 2. Ndi mtundu woyeradi,

    Wophunzitsa cho’nadi.

    Mulungu wawapatsa

    Kuwala kwakedi.

    (KOLASI)

    N’chuma chapadera,

    Otchedwa dzina lanu

    Amakukondani.

    Amalengezadi za inu.

  3. 3. Amasonkhanitsanso,

    Nkhosa zina mwakhama.

    Ndi okhulupirika.

    Kwa Mwanawankhosa.

    (KOLASI)

    N’chuma chapadera,

    Otchedwa dzina lanu

    Amakukondani.

    Amalengezadi za inu.