NYIMBO 28

Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

(Salimo 15)

  1. 1. Ndani angakhale

    bwenzi lanu M’lungu?

    Ndani mungam’khulupirire,

    Angakhale mnzanu?

    Ndi onse amene,

    Amakukondani,

    Amakukhulupirirani,

    Okonda cho’nadi.

  2. 2. Ndani angakhale

    bwenzi lanu M’lungu?

    Ndani angafike kumpando

    wanu wachifumu?

    Ndi onse amene,

    Amakumverani,

    Olemekeza dzina lanu

    Okulambirani.

  3. 3. Timakuuzani,

    Zamumtima mwathu,

    Ndipo timamva

    Kuti tili pafupidi nanu.

    Tifuna kukhala.

    Mabwenzi a inu.

    Palibiretu bwenzi,

    Lomwe lingakuposeni.