NYIMBO 32

Khalani Okhulupirika kwa Yehova

Khalani Okhulupirika kwa Yehova

(Ekisodo 32:26)

  1. 1. Kale tinalitu achisoni,

    Tinali m’chipembedzo chonyenga;

    Koma tinasangalala zedi

    Titamva za Ufumu.

    (KOLASI)

    Yenda ndi Yehova; Usangalale.

    Sangakusiyetu; Yenda m’kuwala.

    Lengeza uthenga Wamtenderewu.

    Ufumu wa Khristu Sudzatha konse.

  2. 2. Timayenda naye nthawi zonse,

    Polalikira kwa anthu onse.

    Pano anthu adzisankhiretu,

    Kumvera M’lungu wathu.

    (KOLASI)

    Yenda ndi Yehova; Usangalale.

    Sangakusiyetu; Yenda m’kuwala.

    Lengeza uthenga Wamtenderewu.

    Ufumu wa Khristu Sudzatha konse.

  3. 3. Mdyerekezi Sitidzamuopa.

    Tidzakhulupirira Yehova.

    Kaya adani angachuluke,

    M’lungu ndi mphamvu yathu.

    (KOLASI)

    Yenda ndi Yehova; Usangalale.

    Sangakusiyetu; Yenda m’kuwala.

    Lengeza uthenga Wamtenderewu.

    Ufumu wa Khristu Sudzatha konse.