NYIMBO 35

“Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

“Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

(Afilipi 1:10)

  1. 1. Kuzindikira kudzatithandiza,

    Kudziwa zoona,

    Kudziwa zomwe ndi zofunika,

    Kuti tizizichita.

    (KOLASI)

    Uzidana ndi choipa.

    Sangalatsa;

    Mtima wa Mulungu,

    Madalitso tidzapeza,

    Tikamachita zofunika.

  2. 2. Palibe chofunika kuposa

    Kulengeza uthenga,

    Kufufuza a njala ya choonadi

    N’kuwaphunzitsa.

    (KOLASI)

    Uzidana ndi choipa.

    Sangalatsa;

    Mtima wa Mulungu,

    Madalitso tidzapeza,

    Tikamachita zofunika.

  3. 3. Tikamachita zofunika,

    Tidzakhala okhutira.

    Mtendere wa Mulungu

    Udzatetezatu maganizo.

    (KOLASI)

    Uzidana ndi choipa.

    Sangalatsa;

    Mtima wa Mulungu,

    Madalitso tidzapeza,

    Tikamachita zofunika.