NYIMBO 49

Tizikondweretsa Mtima wa Yehova

Tizikondweretsa Mtima wa Yehova

(Miyambo 27:11)

  1. 1. M’lungu takulonjezani;

    Kuchita zofuna zanu,

    Tidzagwira ntchito yanu

    Mtima wanu ukondwere.

  2. 2. Kapolo wanu padziko,

    Amalengeza za inu

    Amatipatsa chakudya,

    Kuti tizikumverani.

  3. 3. Mutipatse mzimu wanu,

    Kuti tikhulupirike

    Ndipo tibale zipatso.

    Tizikusangalatsani.