NYIMBO 5

Ntchito Zodabwitsa za Mulungu

Ntchito Zodabwitsa za Mulungu

(Salimo 139)

  1. 1. M’lungu mumandidziwa bwino,

    Ndikagona ndipo ndikadzuka.

    Mumafufuza maganizo anga,

    Mawu ndi njira zanganso

    mumadziwa.

    Munandiona ndili m’mimba,

    Munaonanso mafupa anga.

    Munalemba ziwalo zanga zonse.

    M’lungu wamphamvu

    ndidzakutamandani.

    Nzeru zanu, Mulungu, n’zodabwitsa;

    Zimenezi ndithu ndikudziwa.

    Ndikaopa kupezedwa ndi mdima,

    Mzimu wanu udzandipezabe.

    N’kuti komwe ndingabisale,

    Komwe inu simungandione?

    Kumanda kodi kapena kumwamba

    Mumdima, m’nyanja;

    ayi ndithu kulibe.