NYIMBO 52

Kudzipereka Monga Mkhristu

Kudzipereka Monga Mkhristu

(Aheberi 10:7, 9)

  1. 1. Yehova analengatu

    Chilengedwe chonse,

    Dzikoli ndi mlengalenga,

    Zonsezi ndi zake.

    M’lungu watipatsa moyo

    Wasonyeza kuti

    Ndi woyenera kum’tamanda,

    Ndiponso kum’lambira.

  2. 2. Yesu anabatizidwa

    N’kunena m’pemphero:

    ‘Ndabwera kuti ndichite

    Chifuniro chanu.’

    Anatuluka m’Yo’dano

    Monga wodzozedwa,

    Kuti atumikire M’lungu

    Monga wodzipereka.

  3. 3. Yehova, ife tabwera

    Kukutamandani.

    Tadzipereka kwa inu

    Ndipo tadzikana.

    Yesu munamupereka,

    Monga dipo lathu.

    Tasiyatu zofuna zathu,

    Tizichita za inu.