NYIMBO 54

“Njira Ndi Iyi”

“Njira Ndi Iyi”

(Yesaya 30:20, 21)

  1. 1. Pali njira imene,

    Munaidziwa,

    Njira yamtendere

    Munaiphunzira

    Pamene munamvera

    Mawu a Yesu,

    Ndi njira yopezeka

    M’Mawu a M’lungu.

    (KOLASI)

    Njira yakumoyo ndi yomweyi.

    M’sacheuke m’sapite kumbali!

    Mawu a Mulungu akuti:

    ‘M’sapatuke njira ndi yomweyi.’

  2. 2. Pali njira imene

    Ndi yachikondi,

    Tikaitsatira

    Timaona kuti

    Chikondi cha Mulungu

    ndi chochuluka.

    Njirayi yachikondi;

    Imatikhudza.

    (KOLASI)

    Njira yakumoyo ndi yomweyi.

    M’sacheuke m’sapite kumbali!

    Mawu a Mulungu akuti:

    ‘M’sapatuke njira ndi yomweyi.’

  3. 3. Pali njira ya moyo

    Imodzi yokha.

    Palibe inanso

    M’lungu walonjeza:

    Ndi yokhayi

    Tingapezemo chikondi.

    Njira yakumoyotu

    Ndi imeneyi.

    (KOLASI)

    Njira yakumoyo ndi yomweyi.

    M’sacheuke m’sapite kumbali!

    Mawu a Mulungu akuti:

    ‘M’sapatuke njira ndi yomweyi.’