NYIMBO 66

Lengezani Uthenga Wabwino

Lengezani Uthenga Wabwino

(Chivumbulutso 14:6, 7)

  1. 1. Poyamba sitinkadziwa za Ufumu.

    Pano tikudziwa Mfumu yalonjezo.

    Mwa chifundo ndi chikondi cha Yehova,

    Anaganizira anthu ochimwafe.

    Anakonza zoti Yesu alamule;

    Ufumuwo unali

    woti udzabadwe.

    Komanso kusankha kagulu ka nkhosa,

    Kadzakhale mkwatibwi wa Mwana wake.

  2. 2. Mulungu ankadziwa za uthengawu.

    Pano akufuna anthu audziwe.

    Angelo amakondwa potithandiza

    Kugwira ntchito yolengeza Ufumu.

    Tilitu ndi udindo ndiponso mwayi

    Wom’tamanda ndi kuyeretsa

    dzina lake.

    Tili ndi mwayi wolengeza dzinalo

    Mwa kulalikira uthenga wabwino.