NYIMBO 69

Pitirizani Kulalikira za Ufumu

Pitirizani Kulalikira za Ufumu

(2 Timoteyo 4:5)

  1. 1. Pitani patsogolo ndithu

    Polalikira konse.

    Muthandize anthu ofatsa

    Kukonda choonadi.

    Ndi mwayidi kutumikira.

    Tizikonda ntchito yathu,

    Tizilalikira mwakhama

    Za dzina lake loyera.

    (KOLASI)

    Pitirizani kulalikira

    Padziko lonse.

    Pitirizani kukhala

    Okhulupirikabe.

  2. 2. Tonse tipite patsogolo,

    Abale ndi alongo,

    Odzozedwa ndi nkhosa zina,

    Tizilalikirabe.

    Anthu akufunika kuti

    Amve uthenga wabwino.

    M’lungu amatipatsa mphamvu

    Ndipo sitiopa kanthu.

    (KOLASI)

    Pitirizani kulalikira

    Padziko lonse.

    Pitirizani kukhala

    Okhulupirikabe.