NYIMBO 7

Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

(Yesaya 12:2)

  1. 1. Yehova inu ndi mphamvu yathu,

    Inu ndinu Mpulumutsi wathu.

    Ndife Mboni za uthenga wanu,

    Ngakhale anthu azitinyoza.

    (KOLASI)

    Yehova, thanthwe ndi mphamvu zathu,

    Tilengezabe dzina lanu.

    Yehova inu wamphamvuyonse,

    Pobisala pathu nsanja yathu.

  2. 2. Kuwala kwanu n’kosangalatsa;

    Maso athu aona cho’nadi.

    Malamulo anu tawadziwa,

    Tidzasankhatu Ufumu wanu.

    (KOLASI)

    Yehova, thanthwe ndi mphamvu zathu,

    Tilengezabe dzina lanu.

    Yehova inu wamphamvuyonse,

    Pobisala pathu nsanja yathu.

  3. 3. Chifuniro chanu tichitabe.

    Ngakhale Satana ’matinyoza.

    Kaya atiphe tithandizeni

    Kukhala kumbali yanu M’lungu.

    (KOLASI)

    Yehova, thanthwe ndi mphamvu zathu,

    Tilengezabe dzina lanu.

    Yehova inu wamphamvuyonse,

    Pobisala pathu nsanja yathu.