NYIMBO 83

“Kunyumba ndi Nyumba”

“Kunyumba ndi Nyumba”

(Machitidwe 20:20)

  1. 1. Ife timalalikira

    Kunyumba ndi nyumba.

    Kulikonse nkhosa za M’lungu

    Zikudyetsedwa.

    Tonse, akulu ndi ana,

    Tikulalikira

    Zoti Ufumu wa M’lungu

    Ukulamulira.

  2. 2. Khomo ndi khomo,

    Tinene za chipulumutso.

    Aitane dzina la M’lungu

    Apulumuke.

    Angaitane bwanji

    Dzina sakulidziwa?

    Choncho kunyumba zawo

    Tikawalalikire.

  3. 3. Khomo ndi khomo,

    Tiyeni tikalalikire.

    Asankhe okha kumvera

    Kapena kukana.

    Koma dzina la Yehova

    Tidzalengezabe.

    Tikamatero,

    Tidzapezadi nkhosa zake.