NYIMBO 85

Landiranani

Landiranani

(Aroma 15:7)

  1. 1. Takulandirani inu nonse

    Mwasonkhana kuti m’phunzire.

    Cho’nadi M’lungu amatipatsa;

    Timavomera akamatiitana.

  2. 2. Tikuyamikira abalewa

    Chifukwa amatilandira.

    Ndi amenewa tizikondana,

    Tilandirenso ena odzasonkhana.

  3. 3. Aliyense akuitanidwa,

    Ndi M’lungu kudzaphunzitsidwa.

    M’lungu watikokera kwa Iye.

    Choncho landiranani ndi mtima wonse.