NYIMBO 86

Tikhale Anthu Ophunzitsidwa

Tikhale Anthu Ophunzitsidwa

(Yesaya 50:4; 54:13)

  1. 1. Bwerani mosangalala muphunzire.

    “Bwerani m’dzamwe madzi a moyo.”

    Dzadyeni inu nonse anjala.

    Mudzalandiretu malangizo.

  2. 2. Tisaleketu kusonkhana pamodzi,

    Tiziphunzitsidwa ndi Mulungu.

    Kuno n’kumene kuli abale,

    Kuno kulitu mzimu wa M’lungu.

  3. 3. Lilime lophunzitsidwa choonadi.

    N’losangalatsa kulimvetsera,

    Tipezeke ndi anthu a M’lungu,

    Tizipezeka pamisonkhano.