NYIMBO 87 Bwerani Mudzasangalale Sankhani Zoti Mumvetsere Bwerani Mudzasangalale Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Kukula kwa Zilembo Chithunzi (Aheberi 10:24, 25) 1. Tikukhala m’dziko lomwe n’loipa; Anthu sakudziwa M’lungu. Choncho tifunikatu malangizo, Oti atitsogolere. Misonkhano yathu imathandiza; Kukhala osangalala. Timamvako mawu olimbikitsa Cholinga tisafooke. Sitidzasiya kugwiritsa ntchito; Malamulo a Yehova. Pamisonkhano timalangizidwa; Kukondatu choonadi. 2. Yehova amadziwa bwino zinthu; Zomwe tikufunikira. Tikamasonkhana timasonyeza Kuti timamudalira. Malangizo ochoka kwa akulu, Amatithandiza zedi. Timadziwa kuti sitili tokha, Iwo adzatithandiza. Choncho poyembekezera m’tsogolo, Tisasiye kusonkhana. Tiziphunzira kugwiritsa ntchito Nzeru yochoka kumwamba. (Onaninso Sal. 37:18; 140:1; Miy. 18:1; Aef. 5:16; Yak. 3:17.) Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Bwerani Mudzasangalale IMBIRANI YEHOVA MOSANGALALA Bwerani Mudzasangalale (Nyimbo 87) Chinenero Chamanja cha ku Malawi Bwerani Mudzasangalale (Nyimbo 87) https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1102016887/sign/wpub/1102016887_sign_sqr_xl.jpg sjj 87