NYIMBO 89

Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso

Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso

(Luka 11:28)

  1. 1. Kodi timamveradi Yesu Khristu

    Pa zonse zimene ananena?

    Zomwe anaphunzitsa ndi zabwino.

    Tidalitsidwa tikazimvera.

    (KOLASI)

    Mvera udalitsidwe

    Kuti usangalale.

    Zomwe Mulungu angakuuze,

    Mvera udalitsidwe.

  2. 2. Monga nyumba yomangidwa pathanthwe

    Osati yomangidwa pamchenga.

    Zochita zathu zingatiteteze,

    Kokha ngati Yesu timumvera.

    (KOLASI)

    Mvera udalitsidwe

    Kuti usangalale.

    Zomwe Mulungu angakuuze,

    Mvera udalitsidwe.

  3. 3. Monga mtengo wamumbali mwa madzi

    Umabereka nthawi ’kafika,

    Tikamvera tidzadalitsidwadi,

    Moyo wosatha tidzalandira.

    (KOLASI)

    Mvera udalitsidwe

    Kuti usangalale.

    Zomwe Mulungu angakuuze,

    Mvera udalitsidwe.