NYIMBO 94

Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake

Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake

(Afilipi 2:16)

  1. 1. Yehova Atate, tikuthokoza

    Chifukwa Mawu anu mwatipatsa.

    Munawauziradi;

    Anatimasula.

    Kuwala kwake kwatipatsa nzeru.

  2. 2. Mawu anu ndi amphamvu kwambiri.

    Maganizo n’zolinga ’lekanitsa.

    Ndiponso malamulo,

    Anu n’ngolungama.

    Mfundo zanu zimatitsogolera.

  3. 3. Mawu anu M’lungu, amatikhudza.

    Aneneri anu anali anthu,

    Chonde tithandizeni

    Tikhulupirire.

    Mwatipatsa Mawu, tathokoza Ya.