NYIMBO 96 Baibulo Ndi Chuma Sankhani Zoti Mumvetsere Baibulo Ndi Chuma Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Kukula kwa Zilembo Chithunzi (Miyambo 2:1) 1. Pali buku limene mawu ake Amatibweretsera chimwemwe. Mfundo zake zodabwitsa n’zamphamvu, Limapatsa nzeru owerenga. Bukuli ndi Baibulo loyera. Olilemba anauziridwa. Ankakonda Yehova M’lungu wawo, Mzimu wake unawathandiza. 2. Analemba zokhudza chilengedwe, Mmene M’lungu anachilengera. Analembanso za Paradaiso Ndiponso za mmene anathera. Analemba za mngelo winawake Amene ananyoza Yehova. Anabweretsa mavuto pa anthu Koma Yehova adzapambana. 3. Masiku ano tikusangalala Ufumu wa Mulungu wayamba. Tiuze anthu uthenga wabwino Ndi madalitso omwe abwere. M’Baibulo muli zosangalatsa. Chakudya chochuluka kwambiri. Limatipatsa mtendere wambiri, Tiyesetse kumaliwerenga. (Onaninso 2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21.) Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Baibulo Ndi Chuma IMBIRANI YEHOVA MOSANGALALA Baibulo Ndi Chuma (Nyimbo 96) Chinenero Chamanja cha ku Malawi Baibulo Ndi Chuma (Nyimbo 96) https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1102016896/sign/wpub/1102016896_sign_sqr_xl.jpg sjj 96