Ndilimbitse Chikhulupiriro Changa

Ndilimbitse Chikhulupiriro Changa
  1. 1. Nditani? Ndisankhe njira itiyo? Ndikuganiza.

    Ndinalitu ndi mafunso koma dzikoli

    Silinayankhe.

    Koma ndinayesetsa kufufuza zonse.

    Ndipo ndikayesedwa ndi zoipa

    Ndisachedwetu.

    (KOLASI)

    Ndilimbitse mtima wanga.

    M’pemphe M’lungu, alimbitse

    Chikhulupiriro changa.

    Amandiyankha pondilimbitsa mtima.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.

  2. 2. Zoona satana samatifunira zabwinodi.

    Popanda Yehova sindingakwanitse

    Pandekha n’zovuta.

    Ndimachotsa zoipa ndi zosokoneza.

    Ndimadalira Mulungu wanga,

    Samandisiyatu.

    (KOLASI)

    Ndilimbitse mtima wanga.

    M’pemphe M’lungu, alimbitse

    Chikhulupiriro changa.

    Amandiyankha pondilimbitsa mtima.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Mwina kusinkhasinkha, vesi lina,

    Mawu a m’nyimbo kapena macheza

    Zili ndi yankho la mapemphero anga.

    Ndilimbitse.

    (KOLASI)

    Ndilimbitse mtima wanga.

    M’pemphe M’lungu, alimbitse

    Chikhulupiriro changa.

    Amandiyankhatu pondilimbitsadi mtima.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.

    Ndilimbitse.