Tidzamuimbira YAMBANI Tidzamuimbira Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu 1. Anthu akulira, Akusowa pogwira. Nkhondo, njala, sizikutha. Mafunso ndi ambiri. Nkhawa zikukula, Angathandize n’ndani? Yehova yekha adzatipatsa Dziko labwino zedi. (KOLASI) Atipatsa Mtendere. Madalitso Padzikotu lonse. Tidzamuimbira. 2. Sinkhambakamwatu. Kaya zivute bwanji Yehova M’lungu azitipatsa Mtendere ngati mtsinje. Sitizida nkhawa, Tizisangalala. Podziwa kuti posachedwa Mavutowa atha. (KOLASI) Atipatsa Mtendere. Madalitso Padzikotu lonse. Tidzamuimbira. (VESI LOKOMETSERA) Mu’fumu wa M’lungu Mavuto adzatha. Mtendere konse, imfa kulibe, Anthu adzaimba Mwachisangalalo. (KOLASI) Atipatsa Mtendere. Madalitso Padzikotu lonse. Atipatsa Mtendere. Madalitso Padzikotu lonse. Tidzamuimbira. M’dziko latsopano. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Tidzamuimbira NYIMBO ZATHU Tidzamuimbira Chinenero Chamanja cha ku Malawi Tidzamuimbira https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1014385/univ/art/1014385_univ_sqr_xl.jpg