Chikondi Sichitha

Chikondi Sichitha

(1 Akorinto 13:8)

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Tangoonani;

    Timakondanadi—

    Zomwe n’zosowa m’dzikoli.

    Ndi anzathuwa

    Tikusangalala,

    Sitili mbali ya dziko.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Chikondi sichithadi.

    Chimapiriratu.

    (KOLASI)

    Chikondichitu—

    Yehova n’chikondi.

    Watipatsa.

    Chikondichitu—

    Ndi chofunikadi.

    Tizikondanabe,

    Ndipo tisasiye—

    Chikondichi.

  2. 2. Pena mavuto

    Angatifo’ketse

    N’kuvutika kupirira,

    Koma kupatsa

    Ndi kosangalatsa,

    M’lungu amatitonthoza.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Chikondi sichithadi.

    Chimapiriratu.

    (KOLASI)

    Chikondichitu—

    Yehova n’chikondi.

    Watipatsa.

    Chikondichitu—

    Ndi chofunikadi.

    Tizikondanabe,

    Ndipo tisasiye.

    (KOLASI)

    Chikondichitu—

    Yehova n’chikondi.

    Watipatsa.

    Chikondichitu—

    Ndi chofunikadi.

    Tizikondanabe,

    Ndipo tisasiye—

    Chikondichi,

    Chikondichi,

    Chikondichi.