Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima

Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima

(2 Mafumu 6:16)

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndilitu ndi mantha​—

    Zinthu zikuvuta.

    M’mavuto m’mandithandiza;

    M’makhala pafupi.

    Ndingavutikedi,

    Koma ndikudziwa:

    Ndinu wokhulupirika,

    Mudzanditeteza.

    (KOLASI)

    Yehova, mundithandize

    Ndiziona kuti

    Ndizothekatu kupirira

    Ndilimbedi mtima.

    Tili ndi ambiri

    Kuposa ’daniwa.

    Yehova thandizeni;

    Muwagonjetsadi.

  2. 2. Ndingachite mantha.

    Pandekha n’zovuta.

    Mumanditeteza ndithu;

    Ndidalire inu.

    Mundithandizetu,

    Ndisachite mantha.

    Palibe choti ndiope,

    M’ndende kaya imfa.

    (KOLASI)

    Yehova, mundithandize

    Ndiziona kuti

    Ndizothekatu kupirira.

    Ndilimbedi mtima.

    Tili ndi ambiri;

    Kuposa ’daniwa.

    Yehova thandizeni;

    Muwagonjetsadi.

    (KOLASI)

    Yehova, mundithandize

    Ndiziona kuti

    Ndizothekatu kupirira.

    Ndilimbedi mtima.

    Tili ndi ambiri;

    Kuposa ’daniwa.

    Yehova thandizeni;

    Muwagonjetsadi.

    Yehova thandizeni;

    Muwagonjetsadi.