Tili M’banja la Yehova

Tili M’banja la Yehova
  1. 1. M’dzikoli anthu anaipa,

    Moti sizophweka kupeza mabwenzi.

    Ndinkafunitsitsa n’tapeza anzanga

    Odalirika ndi ondikondadi.

  2. 2. Lero ndawapeza, ndakhutira.

    Gulutu la Yehova lero ndalipeza.

    Anthu ake onse amakondana,

    N’zosangalatsa, ndapeza gulu labwino.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Ndapeza ’bale ndi alongo, ndi makolonso.

    Ndapezatu anzanga osangalatsa

    Ochokera m’mitundu ndi mayiko onse.

    Timakondana, ndife banja limodzi.

  3. 3. Timadziwika ndi chikondi.

    M’gulu lapaderali timasangalala.

    Ndiye tikamakondana kwambiri

    Mulungu wathu amasangalaladi.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Tachokera m’mayiko ndi mitundu yonse.

    Timakondana, ndife banja limodzi.

  4. 4. Tilitu m’gulu lapaderali,

    Yehova watikoka, n’zosangalatsadi.

    Tidzalowatu m’dziko latsopano

    Mongadi banja la padzikotu lonse.

    Monga banjatu limodzidi,

    Limodzi,

    Limodzi.