Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa YAMBANI Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu 1. Pa anthu ochimwafe Palibe amene, Anganenetu, Kuti sanalakwitseko. Lero walakwitsa, Chonde usafooke, Uphunzirepo kanthu. Mulungutu angakuthandize. (KOLASI) Ukagwa, udzuke. Ukhoza kusintha. Ukagwa, dzukatu. Uphunzireponso. Upemphe thandizo, Kwa Mulungu, Wamoyo. Tsimikiza mtima. Iye akulimbitsa. Ukagwa, udzuke. 2. Tsiku lina lafika, Ukudzi’mbabe mlandu. Kale silibwerera, Sungalisinthenso. Usataye mtima. Udalire Yehova. Mawu ake ngamphamvu, Akudzutsa, amakukondabe. (KOLASI) Ukagwa, udzuke. Ukhoza kusintha. Ukagwa, dzukatu. Uphunzireponso. Upemphe thandizo, Kwa Mulungu, Wamoyo. Tsimikiza mtima. Iye akulimbitsa. (VESI LOKOMETSERA) ’Mulungutu ndi wamkulu, Kuposa mitima yathu.’ Iye akutsogolera. Um’dalire. Akudzutsa. (KOLASI) Ukagwa, udzuke. Ukhoza kusintha. Ukagwa, dzukatu. Uphunzireponso. Upemphe thandizo, Kwa Mulungu, Wamoyo. Tsimikiza mtima. Iye akulimbitsa. Ukagwa, udzuke. Ukagwa, dzukatu. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa NYIMBO ZATHU Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa Chinenero Chamanja cha ku Malawi Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1014358/univ/art/1014358_univ_sqr_xl.jpg