JULY 1, 2021
BOLIVIA

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’Chiayimara

Baibulo la Dziko Latsopano Latulutsidwa M’Chiayimara

Pa 27 June 2021, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lapazipangizo zamakono linatulutsidwa m’chinenero cha Chiayimara. M’bale Nelvo Cavalieri wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Bolivia, ndi amene anakamba nkhani yotulutsa Baibuloli. Abale ndi alongo am’mipingo yonse komanso timagulu ta ku Bolivia anaonera pulogalamu yochita kujambulidwa yamsonkhano wotulutsira Baibuloli.

Zokhudza Kutulutsidwa kwa Baibuloli

  • Anthu oposa 1.6 miliyoni, omwe ambiri amakhala m’chigawo cha Nyanja ya Titicaca yomwe ili kumapiri a Andes, amalankhula chilankhulo cha Chiayimara

  • M’dziko la Bolivia anthu amalankhula kwambiri zinenero 36. Ndipo Chiayimara ndi chachiwiri pa zinenero zimene zimalankhulidwa kwambiri ndi anthu am’dzikoli

  • Ofalitsa pafupifupi 2,000 amatumikira m’mipingo ya Chiayimara yoposa 60 ku Argentina, Bolivia, Brazil, Chile ndi Peru

  • Omasulira 6 anagwira ntchito yomasulira Baibuloli kwa zaka 4

Womasulira wina ananena kuti: “Baibuloli ndi mphatso yapadera yomwe Yehova wapereka kwa anthu olankhula Chiayimara. Tsopano anthuwa aziwerenga Baibulo m’chinenero chimene amalankhula ndi kuchimvetsa bwino. Iwo aziona kuti Yehova akulankhula nawo mwachindunji.”

M’bale Mauricio Handal, wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Bolivia anati: “Kungoyambira pamene Baibulo la Malemba Achigiriki linatulutsidwa m’Chiayimara mu 2017, anthu ambiri akhala akuyamikira kuti Baibuloli likumawafika pa mtima. Panopa tili ndi Baibulo lathunthu lomwe linamasuliridwa momveka bwino komanso mmene timalankhulira. Sitikukayikira kuti Baibuloli lithandiza anthu amene aziliwerenga kuti azilimvetsa bwino ndipo koposa zonse liwathandiza kuti ayandikane ndi Yehova yemwe analilemba.”

Tikukhulupirira kuti Baibulo latsopanoli lichititsa abale ndi alongo athu omwe amalankhula Chiayimara kumva mofanana ndi mmene wamasalimo anamvera, yemwe anati: “Ine ndafooka chifukwa cholakalaka chipulumutso chanu, pakuti ndayembekezera mawu anu.”​—Salimo 119:81.