APRIL 7, 2021
CAMBODIA

Baibulo la Dziko Latsopano Linatulutsidwa M’chilankhulo cha Chikambodiya

Baibulo la Dziko Latsopano Linatulutsidwa M’chilankhulo cha Chikambodiya

Pa 3 April 2021, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linatulutsidwa m’chilankhulo cha Chikambodiya. Baibuloli analitulutsa pa zipangizo zamakono ndiponso lochita kusindikizidwa. Abale ndi alongo m’mipingo komanso magulu onse olankhula Chikambodiya, anaonera pulogalamu yonse yochita kujambulidwa ndipo ankaonera kudzera pa intaneti. M’bale Kenji Chichii wa M’komiti ya Nthambi ku Japan * ndi amene anatulutsa Baibuloli.

Chikambodiya chimalankhulidwa ndi anthu pafupifupi 16 miliyoni ndipo ofalitsa oposa 1,100 akutumikira m’gawo la anthu achilankhulochi.

M’bale Masahiro Harada, wa M’komiti ya Nthambi ku Japan, anati: “Sitikukayikira kuti Baibulo limeneli lithandiza anthu kuzindikira makhalidwe abwino a Mulungu monga chikondi komanso chifundo. Tikukhulupirira kuti Baibuloli, lithandiza anthu ambiri amtima wabwino ku Cambodia kuti ayambe kutumikira Yehova ndiponso kumutamanda.”

Ntchito yomasulira Baibuloli inatenga zaka 4 ndipo inagwiridwa ndi omasulira okwanira 6 omwe anagawidwa m’matimu awiri. Mmodzi wa omasulirawa anati: “M’Baibulo latsopanoli sanagwiritse ntchito mawu achikale ovuta kumva. Nditangowerenga, nthawi yomweyo mawu ake anandifika pamtima. Ndinamva ngati mmene anamvera wamasalimo yemwe analemba pa Salimo 139:17 kuti: ‘Kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambiri.’” (Salimo 139:17)

Womasulira wina anati: “Sindikukayikira kuti abale akakawerenga Baibulo latsopanoli, akalimbitsa kwambiri ubwenzi wawo ndi Yehova. Likawathandiza kuona kuti Yehova amawakonda pa nthawi imene akuona kuti ali wokhawokha. Likawathandiza kuona kuti ndi otetezeka pa nthawi imene akumana ndi zoopsa. Baibuloli likawathandiza kukhala ndi mtendere wamumtima pa nthawi imene ali ndi nkhawa. Likawathandiza kukhazika mtima pansi pamene akukumana ndi mayesero.”

Sitikukayikira ngakhale pang’ono kuti Baibulo limeneli lithandiza anthu ambiri kudziwa Mlengi Wamkulu, Yehova komanso kumutamanda ndi kumupatsa ulemu zomwe n’zoyenera kupita kwa iye.—Chivumbulutso 4:11.

^ Nthambi ya Japan ndi yomwe imayang’anira ntchito yolalikira m’dziko la Cambodia.