Mogwirizana ndi akulu a m’mipingo, maofesi a nthambi a ku Rwanda ndi ku Zimbabwe akugwira ntchito yothandiza abale ndi alongo omwe alibe ndalama zokwanira zogulira zinthu zofunika pamoyo chifukwa cha mliri wa colonavairasi.
Ku Rwanda
Pa 2 April 2020, Komiti ya Nthambi ku Rwanda inapempha akulu m’mipingo kuti afufuze komanso athandize abale ndi alongo omwe akhudzidwa ndi mavuto a zachuma chifukwa cha mliriwu. Potsatira zimenezi, akulu m’madera osiyanasiyana m’dzikoli anakonza dongosolo lopereka chakudya ndi zinthu zina zofunika kwa abale ndi alongowa.
Patangodutsa milungu iwiri, ofesi ya nthambi ku Rwanda inakhazikitsa makomiti 31 opereka chithandizo pakagwa mavuto amwadzidzidzi. Makomitiwa anagawa kwa mabanja okhudzidwa zinthu monga ufa, mpunga, nyemba, mchere, shuga ndi mafuta ophikira. Pofika pano, mabanja oposa 7,000 alandira zinthuzi.