Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 29, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Lokonzedwanso Latulutsidwa M’Chikolowesha ndi M’Chisebiya

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Lokonzedwanso Latulutsidwa M’Chikolowesha ndi M’Chisebiya

Pa 25 April 2020, M’bale Mark Sanderson yemwe amatumikira m’Bungwe Lolamulira, analengeza za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso m’zinenero za Chikolewesha ndi Chisebiya. M’baleyu analengeza za kutulutsidwa kwa Mabaibulowa kudzera pavidiyo yojambulidwa kale. Baibulo la Chisebiya linatulutsidwa m’zilembo za Chiromani ndi Chisililiki chomwe.

Pomvera zimene boma laletsa chifukwa cha mliri wa kolonavairasi, mipingo ya ku Bosnia ndi Herzegovina, Croatia, Montenegro, komanso ku Serbia sinakumane pamodzi pamene Mabaibulowa ankatulutsidwa. M’malomwake, msonkhano wapadera unachitika kudzera pa vidiyokomfelensi ndipo abale ndi alongo 12,705 anaonera msonkhanowu.

M’bale wina yemwe anaonera nawo msonkhanowu ananena kuti Baibulo lokonzedwansoli ndi “chinthu chamtengo wapatali” ndiponso anati anamva ‘ngati kuti Yehova akulankhula naye mwachindunji.’ M’bale wina yemwe ndi mkulu mumpingo anati: “Ndikamawerenga Baibulo latsopanoli m’chinenero chomwe ndinabadwa nacho, m’pamene ndizimvetsa kwambiri kuti Yehova amandikonda ndiponso amandisamalira. Komanso ndikamalimbikitsa abale ndi alongo mumpingo, tsopano ndizitha kuwafotokozera momveka bwino zoti Yehova amawakonda kwambiri komanso amawaona kuti ndi ofunika.”

Ntchito yomasulira Mabaibulowa inayamba chakumapeto kwa chaka cha 1996. Mu July 1999, zaka zitatu zisanathe, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’Chikolowesha ndi m’Chisebiya. Kenako patatha zaka 7, mu 2006, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lathunthu linatulutsidwa m’zinenero zonse ziwiri.

Tikukhulupirira kuti Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso m’zinenero za Chikolowesha ndiponso Chisebiya, lomwe ndi lolondola komanso losavuta kumvetsa lipitiriza kuthandiza anthu onse omwe aziliwerenga kuona kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo.”—Aheberi 4:12.