APRIL 19, 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mphepo Yamkuntho ya Seroja Yawononga ku Indonesia ndi ku Timor-Leste

Mphepo Yamkuntho ya Seroja Yawononga ku Indonesia ndi ku Timor-Leste

Malo

Kuzilumba za East Nusa Tenggara kum’mawa kwa Indonesia ndi Timor-Leste

Ngozi yake

  • Pa 4 April 2021, mphepo yamkuntho yotchedwa Seroja inawononga m’madera ambiri komanso anthu anafunika kusamuka m’nyumba zawo

Mmene ngoziyi yakhudzira abale ndi alongo athu

  • Anthu osachepera 236 anachoka m’nyumba zawo

Katundu amene wawonongeka

Indonesia

  • Nyumba 45 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba 8 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongeka pang’ono

Timor-Leste

  • Nyumba 19 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba 10 zinawonongeka kwambiri

Ntchito yothandiza anthu

  • Ku Indonesia, Komiti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi inakhazikitsidwa kuti iyendetse ntchito yothandiza anthu. Komitiyi ikuyendetsa ntchito yokonza Nyumba za Ufumu zimene zinawonongeka komanso nyumba za anthu zimene zinawonongeka kwambiri

  • Oyang’anira madera akugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu polimbikitsa abale ndi alongo amene anakhudzidwa ndi ngoziyi

  • Ngoziyi itangochitika, mwamsanga akulu amumpingo anapezera malo okhala abale ndi alongo omwe anakhudzidwa. Komanso, akuluwa anagawira abale ndi alongo chakudya, madzi ndi zinthu zina zofunikira. Kuwonjezera pamenepo, iwo anathandizanso pa ntchito yokonza nyumba zimene zinawonongeka

  • Ku Timor-Leste, akulu ayamba kale kuyendetsa ntchito yokonza nyumba zimene zinawonongeka komanso kugawa chakudya ndiponso zinthu zina zofunika kwa anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi. Akuluwa apezeranso anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi malo ongoyembekezera oti akhalemo

  • Pogwira ntchitoyi, abale ndi alongo onse akuyesetsa kuchita zinthu mosamala potsatira malangizo opewera mliri wa COVID-19

Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa choti akutithandiza kudzera mu utumiki wothandiza anthu umene abale ndi alongo m’mipingo akuchita.—2 Akorinto 9:13.