MARCH 20, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mwambo Wapadera wa Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Giliyadi

Mwambo Wapadera wa Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Giliyadi

Mwambo wa kalasi nambala 148 ya omaliza maphunziro a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo, sunasiyane kwenikweni ndi wa makalasi ena m’mbuyomu. Komabe mwambo wakalasiyi unali wapadera chifukwa muholo yomwe munachitikira mwambowu munalibe anthu oonerera. Anthu ena onse analumikizidwa kuti aonere mwambowu kudzera pa intaneti. Pamene zinthu si zili bwino pa nkhani ya zaumoyo padziko lonse, mwambowu ndi chitsanzo chimodzi cha zimene gulu la Yehova limachita zinthu zikasintha.

Mwambowu unachitika pa 14 March, 2020, kulikulu la maphunziro la Mboni za Yehova ku Patterson, New York. Tcheyamani wa mwambowu anali M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira. Ophunzira onse omwe anamaliza maphunzirowa anali 55. a

Kutangotsala milungu yochepa kuti mwambowu uchitike, panali malipoti osiyanasiyana ochokera kwa ofalitsa nkhani padziko lonse okhudza kufala kwa mliri wa COVID-19. Monga mmene nkhani yopezeka pagawo la Nkhani pa jw.org inasonyezera, likulu la Mboni za Yehova padziko lonse lakhala likufufuza mosamala kuti lidziwe za kufala kwa mliriwu komanso kupereka malangizo kumipingo yonse, mogwirizana ndi zimene akuluakulu a boma ananena.

Ena mwa malangizowa anali okhudza kuchepetsa chiwerengero cha anthu osonkhana. Poganizira zimenezi komanso mbali zina, Bungwe Lolamulira linasankha kuti pamwambowu pasakhale alendo ochokera kumadera ena. Komanso muholo imene muchitikire mwambowu musakhale anthu oonerera. Banja la Beteli komanso ophunzira a Sukulu ya Giliyadi anasonyeza chitsanzo chabwino pomvera malangizowa.​—Yohane 13:34, 35.

Ngakhale kuti zinthu zinali choncho, alendo a ophunzira a Sukulu ya Giliyadi ndiponso banja la Beteli, analumikizidwa kudzera pa intaneti nthawi yomweyo imene mwambowu unkachitika. Njira imeneyi inathandiza kuti abale ndi alongo oposa 10,000 padziko lonse, kuphatikizapo anzawo ndi achibale a ophunzirawa athe kuonera nawo pulogalamuyi.

Bungwe Lolamulira likufunitsitsa kuti misonkhano ndi zochitika zina zokhudza kulambira, makamaka misonkhano yampingo, zipitirirebe kukhala mbali ya kulambira kwathu ngakhale kuti kuli mliri woopsa wa COVID-19. Chifukwa cha zimenezi, posachedwapa Bungwe Lolamulira lapereka malangizo kumaofesi anthambi padziko lonse a mmene angasinthire misonkhano yampingo mogwirizana ndi mmene zinthu zilili m’dzikolo. Nthawi zina zimenezi zingatanthauze kuti ofalitsa ayenera kumasonkhana m’magulu ang’onoang’ono kapena “kusonkhana” pogwiritsa ntchito njira zamakono monga kulumikizana kudzera pavidiyo. Tikukhulupirira kuti abale ndi alongo padziko lonse apitirizabe kupindula ndi chakudya chauzimu m’mipingo yonse.

Zikuonekeratu kuti palibe chimene chingalepheretse kuti Yehova agwiritse ntchito mphamvu zake potithandiza monga gulu kuti tilimbane ndi vuto lililonse.​—Salimo 18:29.

a Pulogalamu yonse ya mwambo wa Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Giliyadi wa kalasi nambala 148 idzaikidwa pa jw.org mu June 2020.