APRIL 20, 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Ogwira Ntchito pa Beteli pa Dziko Lonse Anachita Mwambo wa Chikumbutso wa 2021

Ogwira Ntchito pa Beteli pa Dziko Lonse Anachita Mwambo wa Chikumbutso wa 2021

Abale ndi alongo ku Warwick, New York, m’dziko la United States anapatsidwa zizindikiro za pa Chikumbutso

Abale ndi alongo a pa Beteli padziko lonse anakonza zoti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu limodzi ndi mipingo yawo pa 27 March 2021. Ena anakamba nkhani ya Chikumbutso pogwiritsa ntchito vidiyokomfelensi.

Mofanana ndi zimene zinachitika mu 2020, atumiki a pa Beteli ya ku United States analandira pulogalamu ya Chikumbutso yochokera ku Likulu la Mboni za Yehova Padziko Lonse. M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhaniyi.

Zithunzi zotsatirazi zikusonyeza m’mene abale ndi alongo otumikira pa Beteli anachitira mwambowu padziko lonse potsatira lamulo la Yesu lakuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”—Luka 22:19.

 

Likulu la Mboni za Yehova pa Dziko Lonse

Nthambi ya Australasia

Omasulira mabuku ku Bangladesh

Ofesi ya Omasulira mabuku ku Cambodia

Nthambi ya ku Cameroon

Nthambi ya ku Central Europe

Nthambi ya ku East Africa

Nthambi ya ku Italy

Nthambi ya ku Kazakhstan

Ofesi ya m’dziko la Nepal

Nthambi ya ku South Africa

Nthambi ya ku Sri Lanka

Nthambi ya ku United States