AUGUST 2, 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Tsiku Lokumbukira Kuti Patha 75 Chichitikireni Msonkhano Waukulu Woyamba Wamayiko

Msonkhano Wosaiwalika Wakuti “Mitundu Yosangalala” Unapereka Chitsanzo cha Misonkhano ya M’tsogolo

Tsiku Lokumbukira Kuti Patha 75 Chichitikireni Msonkhano Waukulu Woyamba Wamayiko

Pomwe timafika pa 4 August 2021, panali patatha zaka 75 chichitikireni msonkhano wakuti “Mitundu Yosangalala,” womwe unali msonkhano waukulu woyamba wamayiko wa Mboni za Yehova. Msonkhanowo unachitika kuyambira pa 4 mpaka pa 11 August, 1946, ku Cleveland, ku Ohio, U.S.A., pa sitediyamu ina komanso holo yomwe inali pafupi ndi sitediyamuyo.

Abale anakonza msonkhanowu nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, yomwe inasautsa dziko lonse lapansi, itangotha kumene. Zochitika za pa msonkhanowu zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe zinachitika pankhondoyo. Pa msonkhanowu panafika abale ndi alongo masauzande ambiri kuchokera padziko lonse. Anthu a mitundu yonse komanso olemera ndi osauka ankachitira zinthu limodzi mosangalala panthawi imene anthu akuda ndi azungu sankachitira zinthu limodzi m’madera ambiri ku United States.

Msonkhano wakuti “Mitundu Yosangalala” unali woyamba kuti Amboni 80,000 asonkhane malo amodzi. Abale ndi alongo athu anasangalala kwambiri kusonkhana pamodzi chifukwa panali patapita nthawi anthu akukhala kwaokha chifukwa cha nkhondo. Pamsonkhanowu panafika alendo 302 ochokera m’mayiko 32. M’bale Nathan H. Knorr anakamba nkhani yamutu wakuti “kalonga wa Mtendere” pa tsiku lomaliza la msonkhanowu lomwe linali Lamlungu.

Kunja kwa sitediyamu yomwe kunachitikira msonkhanowu, kuli chikwangwani choitanira anthu kuti adzamvetsere nkhani ya onse yomwe inakambidwa ndi M’bale Knorr yamutu wakuti “Kalonga wa Mtendere”

Msonkhanowu unayenda bwino kwambiri, komabe mavuto analipo. Pa tsiku loyamba, abale amene ankakonza msonkhanowu anakumana ndi vuto lalikulu kwambiri. Anthu omwe anabwera pamsonkhanowu anali ochuluka kwambiri kuposa anthu amene ankayenera kulowa muholo yomwe unkachitikira. Abale anafunikira kugwiritsa ntchito sitediyamu ina yomwe inali pafupi kuti anthu ena akhalemo pa chigawo chamadzulo cha msonkhanowu chomwe chinayamba nthawi ya 7:45 p.m. Koma pa sitediyamuyi panali poti pakhala masewera awiri ndipo omaliza atha nthawi ya 6:30 p.m.

Koma pamene masewera achiwiri anali mkati, kunagwa mvula ya ziphaliwali yomwe inachititsa kuti anthu omwe ankaonerera atuluke masewerowo asanathe. Koma kenako mvula ija inasiya ndipo kunawala dzuwa zomwe zinachititsa kuti abale ndi alongo okwana 50,000 alowe musitediyamuyo panthawi yake pokonzekera chigawo cha madzulo.

M’bale Knorr akutulutsa buku lakuti “Mulungu Akhale Woona”

Pamsonkhano wa “Mitundu Yosangalala” panatuluka magazini yatsopano ya Galamukani! pamodzi ndi buku lophunzirira Baibulo lamutu wakuti “Mulungu Akhale Woona.” Komanso M’bale Knorr analengeza kuti pali mapulani akuti akulitse nyumba yosindikizira mabuku ya ku Brooklyn, ku New York, U.S.A., komanso maofesi a nthambi a m’mayiko 6.

Chinthu chosangalatsa kwambiri pamsonkhanowu chinali kubatizidwa kwa anthu 2,602. Pa obatizidwawo panali abale 903 komanso alongo 1,699, ndipo anabatizidwa mu nyanja ya Erie yomwe inali pafupi ndi malowo. Zinthu zina zosangalatsa zomwe zinachitika zinali chitsanzo cha Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu komanso nyimbo zomwe zinaimbidwa ndi gulu anthu oimba ndi zida okwana 160.

Abale ndi alongo athu ena akukonzekera kukabatizidwa

Msonkhanowu unapereka chitsanzo cha misonkhano yomwe idzachitike m’tsogolo. Mwachitsanzo, pamsonkhanowu m’pamene panakhazikitsidwa madipatimenti osiyanasiyana monga dipatimenti ya Olandira Alendo, Ofesi ya Tcheyamani, dipatimenti ya Zachipatala, Yoika Zinthu komanso ya Zotayika ndi Zopezeka.

M’bale Ron Little, yemwe pano ndi mkulu mumpingo wa McKeesport ku Pennsylvania, U.S.A., anali ndi zaka 11 pamene ankachita nawo msonkhanowu pamodzi ndi bambo ake komanso mchimwene wake. Ankagona mu galimoto ya bambo ake masiku onse 8 a msonkhanowo.

M’baleyu amakumbukira bwinobwino zomwe zinachitika pamene ankatulutsa magazini ya Galamukani! Iye ananena kuti: “Atatulutsa magazini ya Galamukani!, tinkangozungulirazungulira ili m’mwamba. Ngati sunanyamule magaziniyi m’manja, aliyense ankangofuna atakupatsa.”

M’baleyu yemwe tsopano ali ndi zaka 86, amakumbukiranso kuti anasangalala kwambiri Amboni ambirimbiri atasonkhana malo amodzi. Iye ananena kuti: “Ndimakumbukira kuti ndinkafuna zoti msonkhanowo usathe. Unali msonkhano wabwino kwambiri.”

Timathokoza kwambiri Yehova chifukwa anatidalitsa ndi “misonkhano yopatulika.”​—Levitiko 23:2.

 

Pulogalamu ya msonkhano wa “Mitundu Yosangalala” wa Mboni za Yehova womwe unachitikira ku Cleveland, ku Ohio, U.S.A., kuyambira pa 4 mpaka 11 August, 1946

Magalimoto awiri okhala ndi zokuzira mawu komanso chikwangwani chonena kuti: “Werengani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Consolation.” Chikwangwani china chomwe chili pakhomo la galimoto chikuitanira nkhani ya onse yamutu wakuti “Kalonga wa Mtendere”

Atsikana awiri ndi mayi awo aima kutsogolo kwa galimoto yokhala ndi zokuzira mawu. Atsikanawo akusonyeza kope yoyamba ya Galamukani! yomwe inatulutsidwa mu 1946 pa msonkhano wa “Mitundu Yosangalala.” Mayi awo akusonyeza nyuzipepala ya The Messenger yomwe inkapangidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society

M’bale wajambulitsa chithunzi ndi ana ake awiri. Galimoto yawo ili ndi zikwangwani za nkhani ya onse yakuti “Kalonga wa Mtendere”

Alendo ochokera m’mayiko ena omwe anafika pamsonkhano wa “Mitundu Yosangalala” mu 1946 akulandira zikwangwani zoitanira anthu ku nkhani ya onse yakuti “Kalonga wa Mtendere”

Abale akugwira ntchito ku Dipatimenti Yokonza Chakudya

Anthu omwe anafika pamsonkhano wa “Mitundu Yosangalala” mu 1946 akudya

Anthu omwe anafika pamsonkhanowu anyamula buku limene linali litangotulutsidwa kumene lakuti “Mulungu Akhale Woona”

Abale ali kunja kwa malo omwe kunachitikira msonkhano, ambiri mwa iwo anamangidwapo chifukwa cha chikhulupiriro chawo. M’bale Daniel Sydlik (mzere woyambirira, kumanja kwenikweni), yemwe anadzatumikirapo m’Bungwe Lolamulira, alinso pagululi

Anthu ofuna kubatizidwa akhala kutsogolo

Chithunzi cha m’mwamba cha malo amene panachitikira ubatizo, pa nyanja ya Erie