JANUARY 29, 2021
ERITREA

M’bale Winanso Watulutsidwa M’ndende ku Eritrea

M’bale Winanso Watulutsidwa M’ndende ku Eritrea

Pa 29 January 2021, m’bale wathu wina anatulutsidwa m’ndende atakhalamo kwa zaka zoposa 12. Iye anamangidwa chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira. Posachedwapa pa 4 December 2020, abale enanso okwana 28 anatulutsidwa. Ndife osangalala kwambiri chifukwa cha nkhani yabwino imeneyi. Tipitirizabe kupempherera abale ndi alongo enanso 23 omwe adakali m’ndende ku Eritrea.​—Aheberi 13:3.