Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Zimene Achinyamata Amafunsa

 

Ubwenzi ndi Mulungu

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupemphera?

Kodi pemphero limangothandiza kuti maganizo akhale m’malo, kapena limathandizanso m’njira zina?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupezeka Pamisonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu?

Mlungu uliwonse a Mboni za Yehova amakumana kawiri pa nyumba yomwe amalambirira yotchedwa Nyumba ya Ufumu. Kodi kumeneko kumachitika zotani, nanga mungapindule bwanji ngati mutapezeka pamisonkhano yawo?

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 1: Kuganizira Mozama Mfundo za M’baibulo

Tiyerekeze kuti mwaona chikwama cha ndalama chomwe chikuoneka kuti ndi chakalekale, kodi simungakhale ndi chidwi kuti muone zimene zili mkatimo? Baibulo lili ngati chikwama choterocho. Mumapezeka mfundo zambiri zothandiza.

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 2: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikusangalatsani

Zinthu 5 zomwe zingakuthandizeni kuti muziona zimene mukuwerenga m’Baibulo kuti ndi zenizeni.