ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupemphera?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupemphera?

Kafukufuku wina anasonyeza kuti 80 peresenti ya achinyamata ku America amapemphera, koma hafu ya anthu amenewa ndi amene amapemphera tsiku lililonse. Mwina ena amadzifunsa kuti: ‘Kodi pemphero limangothandiza kuti maganizo akhale m’malo, kapena limathandizanso m’njira zina?’

 Kodi kupemphera n’kutani?

Kupemphera ndi njira yolankhulirana ndi Mlengi wa zinthu zonse. Ndiye tangoganizani, Yehova ndi wapamwamba kuposa anthu m’njira iliyonse, koma “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Ndipo n’zochititsa chidwi kuti Baibulo limatiuza kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.

Kodi mungayandikire bwanji kwa Mulungu?

  • Choyamba, muyenera kupemphera. Imeneyi ndi njira yolankhulira ndi Mulungu.

  • Chachiwiri, muyenera kuphunzira Baibulo. Imeneyi ndi njira imene Mulungu “amalankhulira” ndi inuyo.

Mukamalankhulana ndi Mulungu m’pemphero komanso pophunzira Baibulo, zimathandiza kuti akhale mnzanu wapamtima.

“Kulankhula ndi Yehova, yemwe ndi Wapamwamba Kwambiri m’chilengedwe chonse, ndi mwayi wapadera kwambiri kwa anthu.”​—Jeremy.

“Ndikamapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima zimandithandiza kumva kuti ndi mnzanga wapamtima.​—Miranda.

 Kodi Mulungu amamvetsera mapemphero?

Ngakhale kuti mumakhulupirira Mulungu ndiponso mumapemphera kwa iye, nthawi zina zimakhala zovuta kukhulupirira kuti iye amamvetseradi. Komabe, Baibulo limanena kuti Yehova ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Komanso limakulimbikitsani kuti ‘muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’1 Petulo 5:7.

Ganizirani izi: Kodi inuyo mumakonda kucheza ndi anzanu nthawi zonse? Mukhozanso kuchita chimodzimodzi ndi Mulungu. Muzipemphera kwa iye nthawi zonse, ndipo muzigwiritsa ntchito dzina lake lakuti Yehova. (Salimo 86:​5-7; 88:9) Pa nkhani imeneyi, Baibulo limakulimbikitsani kuti “muzipemphera mosalekeza.”—1 Atesalonika 5:17.

“Ndikamapemphera, ndimakhala ndikulankhula ndi Atate wanga wakumwamba ndipo ndimawakhuthulira zonse zamumtima mwanga.”​—Moises.

“Yehova ndimamuuza chilichonse chakukhosi kwanga ngati mmene ndingachitire ndi mayi anga kapena mnzanga wapamtima.”​—Karen.

 Kodi ndinganene nkhani ziti popemphera?

Baibulo limanena kuti: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tikhoza kumapempherera mavuto athu? Inde, ndipo Baibulo limanena kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.”—Salimo 55:22.

Komabe, mukamapemphera kwa Mulungu, muzimuuzanso zinthu zina osati mavuto anu okhaokha. Mtsikana wina dzina lake Chantelle ananena kuti: “Sindinganene kuti Yehova ndi mnzanga wapamtima ngati ndimangomupempha kuti andithandize. Ndimaona kuti ndiyenera kuyamba ndi kumuthokoza pa zinthu zambiri zimene amandichitira.”

Ganizirani izi: Kodi inuyo mumayamikira zinthu ziti pamoyo wanu? Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene mungayamikire Yehova lero?

“Tikhoza kupereka pemphero loyamikira Yehova ngakhale pa zinthu zing’onozing’ono monga maluwa okongola.”​—Anita.

“Ganizirani chinthu china cha m’chilengedwe chimene chimakugometsani kapena vesi limene limakufikani pamtima kenako mumuthokoze Yehova.”​—Brian.