Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Akazi Otchulidwa m’Baibulo?

Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Akazi Otchulidwa m’Baibulo?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limafotokoza za akazi ambiri omwe anachita zinthu zosiyanasiyana pa moyo wawo ndipo ifeyo tingaphunzirepo kanthu pa zimene anachitazo. (Aroma 15:4; 2 Timoteyo 3:16, 17) Nkhaniyi ikungofotokoza mwachidule za ena mwa akazi otchulidwa m’Baibulo. Ambiri mwa akazi amenewa anasonyeza chitsanzo chabwino choti tingatsanzire. Koma zimene ena anachita ndi zotichenjeza.—1 Akorinto 10:11; Aheberi 6:12.

  Abigayeli

 Kodi anali ndani? Anali mkazi wa munthu wina wolemera koma wankhanza dzina lake Nabala. Koma Abigayeli anali wanzeru, wodzichepetsa, wokongola ndiponso anali ndi makhalidwe omwe Mulungu amasangalala nawo.—1 Samueli 25:3.

 Kodi anachita zotani? Anachita zinthu mwanzeru komanso mozindikira poteteza banja lake ku tsoka. Iye ndi Nabala ankakhala kudera limene kunabisala Davide, yemwe anadzakhala mfumu. Davide ndi anyamata ake ali kumeneko, ankateteza nkhosa za Nabala kuti zisabedwe. Koma Davide atatumiza anyamata ake kuti akapemphe chakudya kwa Nabala, Nabalayo anawakaniza mwamwano. Davide anakwiya kwambiri ndi zimenezi, moti iyeyo ndi anyamata akewo anakonza zoti akaphe Nabala limodzi ndi amuna onse a m’banja lake.—1 Samueli 25:10-12, 22.

 Abigayeli anachita zinthu mwachangu atamva zomwe mwamuna wake wachita. Anatenga chakudya n’kupatsira anyamata ake kuti akapereke kwa Davide ndipo naye anawatsatira kuti akapepese kwa Davide. (1 Samueli 25:14-19, 24-31) Davide ataona mphatso zomwe Abigayeli anabweretsa, kudzichepetsa kwake komanso malangizo ake anzeru, anazindikira kuti Mulungu wagwiritsa ntchito Abigayeli kuti amuthandize kusintha maganizo owononga nyumba ya Nabala. (1 Samueli 25:32, 33) Pasanapite nthawi, Nabala anamwalira ndipo Abigayeli anakhala mkazi wake wa Davide.—1 Samueli 25:37-41.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Abigayeli anachita? Ngakhale kuti Abigayeli anali wokongola komanso wachuma, sankadziona kukhala wofunika kuposa ena. Pofuna kukhazikitsa mtendere analolera kupepesa pa zinthu zoti sanalakwitse ndi iyeyo. Komanso nkhani imene inachitikayi inali yovuta kwambiri, koma anaithetsa modekha, mwaulemu, molimba mtima komanso mwanzeru.

  Debora

 Kodi anali ndani? Anali mneneri wamkazi amene Yehova, Mulungu wa Isiraeli, ankamugwiritsa ntchito akafuna kuuza anthu ake zoyenera kuchita. Mulungu ankamugwiritsanso ntchito poweruza milandu ya pakati pa Aisiraeli.—Oweruza 4:4, 5.

 Kodi anachita zotani? Debora anachita zinthu molimba mtima pothandiza olambira Mulungu. Mothandizidwa ndi Yehova, analamula Baraki kuti atsogolere gulu lankhondo la Aisiraeli pokagonjetsa Akanani omwe ankawapondereza. (Oweruza 4:6, 7) Baraki atamupempha Debora kuti apitire limodzi, Debora anavomera mopanda mantha.—Oweruza 4:8, 9.

 Mulungu atathandiza Aisiraeli kugonjetsa adani awo, Debora anapeka nyimbo yofotokoza zomwe zinachitikazo ndipo iyeyo ndi Baraki anaimbira limodzi. Nyimboyo inafotokoza zomwe mkazi winanso wolimba mtima dzina lake Yaeli anachita pothandizira kuti Akanani agonje.—Oweruza, chaputala 5.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Debora anachita? Debora anali wodzipereka komanso wolimba mtima. Ankalimbikitsa ena kuti azichita zinthu zomwe Mulungu amasangalala nazo. Anthuwo akamvera, Debora ankawayamikira.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Debora, werengani nkhani yakuti “Ine Ndinauka Monga Mayi mu Isiraeli.”

  Delila

 Kodi anali ndani? Anali mkazi amene anali pa chibwenzi ndi woweruza Samisoni wa ku Isiraeli.—Oweruza 16:4, 5.

 Kodi anachita zotani? Analandira ndalama kwa Afilisiti n’cholinga choti apereke Samisoni m’manja mwawo, yemwe pa nthawiyo Mulungu ankamugwiritsa populumutsa Aisiraeli kwa Afilisiti. Chifukwa cha mphamvu zodabwitsa zimene Samisoni anali nazo, Afilisiti ankalephera kumugonjetsa. (Oweruza 13:5) Kenako Afilisiti ananyengerera Delila kuti awathandize kugonjetsa Samisoni.

 Afilisiti anamulonjeza Delila kuti adzamupatsa ndalama akawauza chimene chinkachititsa kuti Samisoni akhale ndi mphamvu zochuluka. Delila anavomera ndalamazo ndipo atamunyengera Samisoni maulendo ambiri kuti aulule, Samisoni anaulula komwe kunkachokera mphamvuzo. (Oweruza 16:15-17) Kenako Delila anakauza Afilisiti za nkhaniyi ndipo iwo anagwira Samisoni n’kukamuika m’ndende.—Oweruza 16:18-21.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Delila anachita? Zimene Delila anachita ndi chenjezo kwa ife. Chifukwa cha mtima wadyera, anachita zinthu zachinyengo, zosakhulupirika komanso zodzikonda popereka mtumiki wa Yehova m’manja mwa adani.

  Esitere

 Kodi anali ndani? Anali mtsikana wachiyuda yemwe Mfumu Ahasiwero ya ku Perisiya anamusankha kukhala mkazi wake.

 Kodi anachita zotani? Anagwiritsa ntchito udindo wake poteteza anthu a mtundu wake kuti asaphedwe. Esitere anamva kuti pakhazikitsidwa lamulo komanso tsiku loti Ayuda onse okhala m’chigawo cha Perisiya aphedwe. Hamani, yemwe anali nduna yaikulu yapanyumba ya mfumu ndi amene anakonza chiwembuchi. (Esitere 3:13-15; 4:1, 5) Mothandizidwa ndi msuweni wake Moredekai, Esitere analolera kuika moyo wake pachiswe poulula za chiwembuchi kwa mwamuna wake, Mfumu Ahasiwero. (Esitere 4:10-16; 7:1-10) Ahasiwero analola kuti Esitere ndi Moredekai akhazikitsenso lamulo lina lopatsa mphamvu Ayuda kuti adziteteze. Ndipo izi zinathandiza kuti Ayuda agonjetse adani awowo.—Esitere 8:5-11; 9:16, 17.

Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Esitere anachita? Esitere ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kulimba mtima komanso kudzichepetsa. (Salimo 31:24; Afilipi 2:3) Ngakhale kuti anali wokongola komanso anali ndi udindo, ankapempha malangizo komanso thandizo kwa ena. Pamene ankalankhula ndi mwamuna wake, Esitere ankachita zinthu mwanzeru ndiponso mwaulemu, koma molimba mtima. Ndipo pa nthawi imene moyo wa Ayuda unali pangozi, Esitere analimba mtima kudzidziwikitsa kuti nayenso ndi Myuda.

  Hava

 Kodi anali ndani? Anali mkazi woyamba kulengedwa komanso woyamba kutchulidwa m’Baibulo.

 Kodi anachita zotani? Hava sanamvere lamulo lomveka bwino lomwe Mulungu anapereka. Mofanana ndi mwamuna wake Adamu, Hava anali wangwiro komanso anapatsidwa ufulu wosankha zochita. Analinso ndi mwayi wosonyeza makhalidwe omwe Mulungu ali nawo, makhalidwe ngati chikondi komanso nzeru. (Genesis 1:27) Hava ankadziwa kuti Mulungu anauza Adamu kuti akadzangodya chipatso cha mtengo winawake, adzafa. Koma Satana anamupusitsa pomuuza kuti sadzafa ndipo iye anakhulupiriradi. Hava anakhulupirira bodza limene Satana anamunamiza loti adzakhala ndi moyo wabwino kwambiri ngati atapanda kumvera Mulungu. Iye anadya chipatsocho n’kukapatsanso mwamuna wake ndipo nayenso anadya.—Genesis 3:1-6; 1 Timoteyo 2:14.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Hava anachita? Zimene Hava anachita ndi zotichenjeza kudziwa mavuto amene amakhalapo tikamangoganizira zinthu zosayenera. Iye anayamba kulakalaka kwambiri zinthu zomwe sizinali zake ndipo zinachititsa kuti aphwanye lamulo lomwe Mulungu anawapatsa.—Genesis 3:6; 1 Yohane 2:16.

  Hana

 Kodi anali ndani? Anali mkazi wa Elikana komanso mayi ake a Samueli yemwe anadzakhala mneneri wodziwika bwino mu Isiraeli.—1 Samueli 1:1, 2, 4-7.

 Kodi anachita zotani? Pa nthawi imene Hana anali wosabereka, ankapempha Mulungu kuti amutonthoze. Mwamuna wake anali ndi akazi awiri, Penina ndi iyeyo. Penina anali ndi ana pamene Hana anakhala wopanda mwana kwa nthawi yaitali. Penina ankangokhalira kunyoza Hana koma iye ankapemphera kwa Mulungu kuti azimulimbikitsa. Hana analonjeza Mulungu kuti ngati angamupatse mwana wamwamuna, adzamupereka kwa iye kuti azikatumikira pa chihema. Chihema chinali tenti yomwe Aisiraeli ankalambiriramo, ndipo akamasamuka ankainyamula.—1 Samueli 1:11.

 Mulungu anayankha pemphero la Hana ndipo anabereka Samueli. Pokwaniritsa lonjezo lake, Hana anam’tenga Samueli adakali wamng’ono n’kukamupereka kuchihema kuti azikatumikirako. (1 Samueli 1:27, 28) Chaka chilichonse, Hana ankamusokera Samueli malaya akunja odula manja n’kukamupatsa. Patapita nthawi, Mulungu anadalitsa Hana pomupatsa ana ena 5, aamuna atatu ndi aakazi awiri.—1 Samueli 2:18-21.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Hana anachita? Hana anakwanitsa kupirira mayesero chifukwa choti ankapemphera mochokera pansi pamtima. Ndipo pemphero lake loyamikira lomwe lili pa 1 Samueli 2:1-10 limasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Mulungu.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Hana, werengani nkhani yakuti “Anapemphera Kuchokera Pansi pa Mtima.”

  •   Kuti mudziwe chifukwa chimene Mulungu ankalolera anthu akale kuchita mitala, werengani nkhani yakuti “Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?

  Yaeli

 Kodi anali ndani? Anali mkazi wa Hiberi, yemwe sanali Mwisiraeli. Yaeli anachita zinthu mopanda mantha pothandiza anthu a Mulungu.

 Kodi anachita zotani? Yaeli anachita zinthu molimba mtima kwambiri pamene Sisera, yemwe anali mkulu wa asilikali a Akanani, analowa mu hema wake. Sisera atagonja pa nkhondo yomenyana ndi Aisiraeli anayamba kufunafuna malo oti abisale. Yaeli anamuitanira mu hema wake kuti abisale komanso apumule. Sisera ali m’tulo, Yaeli anamupha.—Oweruza 4:17-21.

 Zimene Yaeli anachitazi zinakwaniritsa ulosi umene Debora analosera kuti: “Yehova adzapereka Sisera m’manja mwa munthu wamkazi.” (Oweruza 4:9) Zimene anachitazi zinapangitsa kuti anthu azimutamanda kuti ndi “wodalitsika pakati pa akazi onse.”—Oweruza 5:24.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yaeli anachita? Yaeli anachita zinthu modzipereka komanso molimba mtima. Zimene anachita zimasonyeza kuti Mulungu akhoza kugwiritsa ntchito aliyense kuti akwaniritse zimene walosera.

  Yezebeli

 Kodi anali ndani? Anali mkazi wa Ahabu, Mfumu ya Isiraeli. Yezebeli sanali Mwisiraeli ndiponso sankalambira Yehova. Iye ankalambira Baala, mulungu wa Akanani.

 Kodi anachita zotani? Mfumukazi Yezebeli anali wonyada, wopanda chifundo komanso wankhanza. Iye ankalimbikitsa anthu kuti azilambira Baala komanso kuti azichita zachiwerewere monga mbali ya kulambira kwawo. Pamene ankachita zimenezi, ankayesetsanso kuti athetse zolambira Mulungu woona, Yehova.—1 Mafumu 18:4, 13; 19:1-3.

 Yezebeli akafuna chinthu ankalolera kupha anthu kapena kugwiritsa ntchito bodza kuti apeze chomwe akufunacho. (1 Mafumu 21:8-16) Mogwirizana ndi zomwe Mulungu ananeneratu, Yezebeli anafa imfa yomvetsa chisoni komanso sanaikidwe m’manda.—1 Mafumu 21:23; 2 Mafumu 9:10, 32-37.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yezebeli anachita? Zimene Yezebeli anachita ndi chenjezo kwa ife. Popeza kuti anali wamakhalidwe oipa kwambiri ndiponso ankachita zinthu mwachinyengo kuti apeze zomwe akufuna, anthu amagwiritsa ntchito dzina lake ponena za mkazi wopanda manyazi, wachiwerewere komanso wopanga zinthu zoipa mopanda mantha.

  Leya

 Kodi anali ndani? Anali mkazi woyamba wa Yakobo. Mng’ono wake Rakele ndi amene anali mkazi wachiwiri.—Genesis 29:20-29.

 Kodi anachita zotani? Leya anaberekera Yakobo ana aamuna 6. (Rute 4:11) Poyamba Yakobo ankafuna kukwatira Rakele osati Leya. Koma Labani, bambo wa atsikanawa, ndi amene anakonza zoti Yakobo akwatire Leya m’malo mwa Rakele. Yakobo atazindikira kuti amupusitsa pomupatsa Leya, anapita kukafunsa Labani. Iye anayankha kuti mwambo wawo sumalola kuti wamng’ono ayambe kukwatiwa wamkulu asanakwatiwe. Patangodutsa mlungu umodzi, Yakobo anakwatira Rakele.—Genesis 29:26-28.

 Yakobo ankakonda kwambiri Rakele kuposa Leya. (Genesis 29:30) Zimenezi zinachititsa kuti Leya azichitira nsanje m’bale wakeyo n’kumachita zinthu za mpikisano kuti mwina Yakobo angayambe kumukonda iyeyo. Mulungu anadziwa mmene Leya ankamvera ndipo anamudalitsa ndi ana 7, aamuna 6 ndi wamkazi mmodzi.—Genesis 29:31.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Leya anachita? Leya ankapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize ndipo, ngakhale kuti anali ndi mavuto a m’banja, ankaonabe kuti Mulungu akumuthandiza. (Genesis 29:32-35; 30:20) Ngakhale kuti pa nthawi inayake Mulungu ankalola mwamuna kukhala ndi akazi angapo, nkhani ya Leya imasonyeza mavuto amene amabwera chifukwa cha mitala. Zimene Mulungu amafuna ndi zoti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi.—Mateyu 19:4-6.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Leya, werengani nkhani yakuti “Moyo Wawo Unali Wovuta Koma ‘Anamanga Nyumba ya Isiraeli.’

  •   Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu ankalola anthu akale kuchita mitala, werengani nkhani yakuti “Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?

  Marita

 Kodi anali ndani? Anali m’bale wake wa Lazaro ndi Mariya, ndipo atatu onsewa ankakhala m’mudzi wa Betaniya pafupi ndi Yerusalemu.

 Kodi anachita zotani? Marita ankacheza kwambiri ndi Yesu ndipo Yesu “anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.” (Yohane 11:5) Marita ankakonda kuchereza alendo. Nthawi ina Yesu atabwera kunyumba kwawo, Mariya anakhala pansi pafupi ndi Yesu n’kumamumvetsera, pamene Marita anali atatanganidwa ndi kukonza chakudya. Marita atadandaulira Yesu kuti Mariya sakumuthandiza ntchito, Yesu anamuthandiza kudziwa zomwe zinali zoyenera kuchita pa nthawiyo.—Luka 10:38-42.

 Lazaro atadwala, Marita ndi mchemwali wake anatumiza uthenga kwa Yesu, chifukwa ankakhulupirira kuti Yesu akhoza kumuchiritsa. (Yohane 11:3, 21) Koma Lazaro anamwalira. Zimene Marita anakambirana ndi Yesu zimasonyeza kuti Marita anali ndi chikhulupiriro choti akufa adzauka komanso kuti Yesu anali ndi mphamvu zoukitsa Lazaro.—Yohane 11:20-27.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Marita anachita? Marita ankakonda kuchereza alendo. Atapatsidwa malangizo, anatsatira mosanyinyirika. Marita sankachita manyazi kufotokoza mmene ankamvera komanso zimene ankakhulupirira.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Marita, werengani nkhani yakuti “Ndimakhulupirira.”

  Mariya (mayi ake a Yesu)

 Kodi anali ndani? Anali mtsikana wachiyuda ndipo pa nthawi imene ankabereka Yesu n’kuti adakali namwali chifukwa Mulungu anachititsa kuti atenge pakati mozizwitsa.

 Kodi anachita zotani? Mariya anavomera modzichepetsa kuchita zimene Mulungu anamuuza. Pa nthawi imene anali pachibwenzi ndi Yosefe, mngelo anabwera kudzamuuza kuti adzakhala ndi pakati ndipo adzabereka Mesiya yemwe anthu anali atamuyembekezera kwa nthawi yaitali. (Luka 1:26-33) Mariya anavomera ndi mtima wonse. Yesu atabadwa, Mariya ndi Yosefe anaberekanso ana ena aamuna 4 ndi aakazi awiri. Izi zikusonyeza kuti Mariya sanakhale namwali moyo wake wonse. (Mateyu 13:55, 56) Ngakhale kuti anagwiritsidwa ntchito mwapadera chonchi, Mariya sanaganizepo zoti azipatsidwa ulemu wapadera pa nthawi imene Yesu ankachita utumiki wake, kapenanso pamene anali mumpingo wachikhristu woyambirira.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Mariya anachita? Mariya anali mkazi wokhulupirika ndipo anavomera mochokera pansi pamtima udindo waukulu womwe anapatsidwa. Komanso ankadziwa bwino Malemba moti zikuoneka kuti pamene ankafotokoza mawu omwe ali pa Luka 1:46-55, anagwira mawu a m’Malemba maulendo pafupifupi 20.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Mariya, werengani nkhani yakuti “Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?”

  Mariya (mlongo wake wa Marita ndi Lazaro)

 Kodi anali ndani? Anali m’bale wake wa Lazaro ndi Mariya, ndipo onse ankakonda kucheza ndi Yesu.

 Kodi anachita zotani? Mobwerezabwereza Mariya anasonyeza kuti ankalemekeza kwambiri Yesu monga mwana wa Mulungu. Iye ankakhulupirira kuti Yesu akanatha kuchiritsa mchimwene wake Lazaro kuti asamwalire ndipo analipo nthawi imene Yesu ankaukitsa Lazaro. Nthawi ina mchemwali wake Marita anamuimba mlandu kuti Mariyayo wasankha kumvetsera Yesu m’malo moti azikamuthandiza ntchito zapakhomo. Koma Yesu anayamikira Mariya chifukwa choti ankaona kuti zinthu zauzimu ndiye zofunika kwambiri.—Luka 10:38-42.

 Pa nthawi ina Mariya anasonyeza mtima wochereza m’njira yapadera kwambiri chifukwa anathira Yesu m’mutu “mafuta onunkhira okwera mtengo.” (Mateyu 26:6, 7) Anthu ena ankaona kuti zimene Mariya akuchita n’kuwononga zinthu. Koma zimene Yesu analankhula zinasonyeza kuti Mariya sanalakwitse. Iye ananena kuti: “Kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwe m’dziko lonse, anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzam’kumbukira.”—Mateyu 24:14; 26:8-13.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Mariya anachita? Mariya anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ankaona kuti kulambira Mulungu ndi kofunika kwambiri kuposa zinthu zina zonse. Komanso analolera kuwononga ndalama zambiri kuti alemekeze Yesu.

  Mariya Mmagadala

 Kodi anali ndani? Anali wophunzira wokhulupirika wa Yesu Khristu.

 Kodi anachita zotani? Mariya Mmagadala anali mmodzi mwa akazi ambiri omwe ankayenda limodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. Iye ankagwiritsa ntchito chuma chake posamalira Yesu ndi atumwi akewo. (Luka 8:1-3) Mariya anakhala wotsatira wa Yesu mpaka kumapeto kwa utumiki wake ndipo analiponso pamene Yesu ankaphedwa. Iye anali ndi mwayi wokhala mmodzi mwa anthu oyamba kumuona Yesu ataukitsidwa.—Yohane 20:11-18.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Mariya Mmagadala anachita? Mariya anasonyeza kuwolowa manja pothandizira utumiki wa Yesu ndi chuma chake komanso anakhalabe wotsatira wa Yesu moyo wake wonse.

  Miriamu

 Kodi anali ndani? Anali mlongo wake wa Mose ndi Aroni. Ndipo ndi mkazi woyamba m’Baibulo kutchulidwa kuti anali mneneri.

 Kodi anachita zotani? Monga mneneri, anali ndi udindo wopereka mauthenga a Mulungu kwa anthu. Miriamu anali ndi udindo waukulu mu Isiraeli ndipo Mulungu atagonjetsa gulu la nkhondo la Aiguputo pa Nyanja Yofiira, iye anaimbira limodzi ndi azibambo nyimbo yotamanda Mulungu.—Ekisodo 15:1, 20, 21.

 Patapita nthawi, Miriamu ndi Aroni anayamba kulankhula zinthu zambirimbiri zodzudzula Mose ndipo zimaoneka kuti anachita zimenezi chifukwa cha kunyada komanso nsanje. Koma Mulungu “anali kumvetsera,” ndipo anawadzudzula mwamphamvu. (Numeri 12:1-9) Kenako Mulungu anakantha Miriamu ndi khate chifukwa choti ndi amene anayambitsa kulankhula zoipazo. Mose anachonderera Mulungu kuti amukhululukire Miriamu ndipo anamuchiritsadi. Miriamu atakhala kunja kwa msasa masiku 7, analoledwa kubwereranso.—Numeri 12:10-15.

 Baibulo limasonyeza kuti Miriamu anamvera malangizo omwe anapatsidwa. Patapita zaka zambiri, Mulungu anatchula za udindo wake wapadera pamene anakumbutsa Aisiraeli kuti: “Ndinakutumizirani Mose, Aroni ndi Miriamu kuti akutsogolereni.”—Mika 6:4.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Miriamu anachita? Nkhani ya Miriamu imasonyeza kuti Mulungu amamvetsera zomwe anthu ake akukambirana kapena zimene akunena zokhudza anzawo. Ikutiphunzitsanso kuti ngati tikufuna kusangalatsa Mulungu, tiyenera kupewa kunyada komanso nsanje, zomwe zingatichititse kuti tiyambe kunena zinthu zoipitsa mbiri ya ena.

  Rakele

 Kodi anali ndani? Anali mwana wamkazi wa Labani komanso mkazi amene Yakobo ankamukonda kwambiri.

 Kodi anachita zotani? Rakele anakwatiwa ndi Yakobo ndipo anamuberekera ana awiri aamuna. Anawa ndi ena mwa ana amene anadzakhala mitu ya mabanja a mafuko 12 Aisiraeli. Rakele anakumana ndi Yakobo pamene ankasamalira nkhosa za bambo ake. (Genesis 29:9, 10) Rakele “anali chiphadzuwa” poyerekezera ndi mkulu wake Leya.—Genesis 29:17.

 Yakobo anakopeka ndi Rakele, moti anavomera kugwira ntchito kwa zaka 7 kuti amukwatire. (Genesis 29:18) Poyamba Labani anapusitsa Yakobo pomuchititsa kuti akwatire Leya, koma pambuyo pake anamulola kuti akwatire Rakele.—Genesis 29:25-27.

 Yakobo ankakonda kwambiri Rakele ndi ana ake awiri kuposa mmene ankakondera Leya ndi ana ake. (Genesis 37:3; 44:20, 27-29) Zimenezi zinachititsa kuti akazi awiriwa asamagwirizane.—Genesis 29:30; 30:1, 15.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Rakele anachita? Rakele anapirira mavuto omwe ankakumana nawo m’banja ndipo sankakayikira kuti Mulungu amva mapemphero ake. (Genesis 30:22-24) Nkhani yake imasonyeza mavuto amene amakhalapo m’banja chifukwa cha mitala. Zomwe Rakele anakumana nazo zikusonyeza kuti lamulo lomwe Mulungu anakhazikitsa poyamba, loti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi yekha, ndi labwino kwambiri.—Mateyu 19:4-6.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Rakele, werengani nkhani yakuti “Moyo Wawo Unali Wovuta Koma ‘Anamanga Nyumba ya Isiraeli.’

  •   Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu ankalola kuti anthu akale azichita mitala, werengani nkhani yakuti “Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?

  Rahabi

 Kodi anali ndani? Anali hule ndipo ankakhala mumzinda wa Yeriko, koma kenako anayamba kulambira Yehova Mulungu.

 Kodi anachita zotani? Rahabi anabisa Aisiraeli awiri omwe anapita kukafufuza za dzikolo. Anachita zimenezi chifukwa anamva mmene Yehova, Mulungu wa Isiraeli, anapulumutsira anthu ake ku Igupto komanso m’manja mwa Aamori.

 Rahabi anathandiza anthuwo ndipo anawapempha kuti adzapulumutse moyo wake ndi wa abale ake Aisiraeli akamadzawononga mzinda wa Yeriko. Anthuwo anagwirizana nazo, koma anamuuza kuti pali zimene nayenso akufunika kuchita kuti zimenezi zitheke. Anamuuza kuti asunge chinsinsi, iyeyo limodzi ndi abale ake onse asadzatuluke m’nyumba Aisiraeli akamadzawononga mzindawo, komanso kuti apachike chingwe chofiira pawindo la nyumba yake kuti adzaizindikire mosavuta. Rahabi anatsatira malangizo onsewa, ndipo iyeyo ndi abale ake anapulumuka pamene Aisiraeli ankawononga mzinda wa Yeriko.

 Patapita nthawi Rahabi anakwatiwa ndi Mwisiraeli ndipo anakhala kholo la Mfumu Davide komanso Yesu Khristu.—Yoswa 2:1-24; 6:25; Mateyu 1:5, 6, 16.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Rahabi anachita? Baibulo limafotokoza kuti Rahabi ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya chikhulupiriro. (Aheberi 11:30, 31; Yakobo 2:25) Nkhani yake imasonyeza kuti Mulungu amakhululuka komanso alibe tsankho ndipo amadalitsa anthu omwe amamukhulupirira mosatengera komwe amachokera kapena zomwe ankachita m’mbuyo.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Rahabi, werengani nkhani yakuti “Anaonedwa ‘Ngati Wolungama Chifukwa cha Ntchito Zake.’

  Rabeka

 Kodi anali ndani? Anali mkazi wa Isaki ndipo anabereka ana amapasa, Esau ndi Yakobo.

 Kodi anachita zotani? Rabeka anachita zimene Mulungu amafuna ngakhale pa nthawi imene kuchita zimenezi kunali kovuta. Rabeka atatunga madzi pachitsime, munthu wina anamupempha kuti amugawireko madzi akumwa. Iye anamupatsadi mofulumira ndipo anadzipereka kutungiranso madzi akumwa ngamila za munthuyo. (Genesis 24:15-20) Munthuyu anali mtumiki wa Abulahamu ndipo anayenda mtunda wautali akufufuza munthu woti akhale mkazi wa Isaki, mwana wa Abulahamu. (Genesis 24:2-4) Mtumikiyu anapempha kuti Mulungu amudalitse. Choncho ataona kuti Rabeka ndi wolimbikira ntchito komanso wochereza, mtumikiyu anadziwa kuti Mulungu wayankha pemphero lake ndipo wasankha Rabeka kukhala mkazi wa Isaki.—Genesis 24:10-14, 21, 27.

 Mtumikiyo atauza Rabeka za cholinga cha ulendo wakewo, Rabeka anavomera kuti apita naye limodzi kuti akakhale mkazi wa Isaki. (Genesis 24:57-59) Patapita nthawi Rabeka anabereka ana amuna awiri amapasa. Mulungu ananeneratu kuti Esau, yemwe ndi wamkulu adzatumikira wamng’ono, Yakobo. (Genesis 25:23) Pamene Isaki ankakonza zoti adalitse Esau monga woyamba kubadwa, Rabeka anachita zinthu zothandiza kuti madalitsowo apite kwa Yakobo, mogwirizana ndi zimene Mulungu ankafuna.—Genesis 27:1-17.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Rabeka anachita? Rabeka anali wodzichepetsa, wolimbikira ntchito komanso wodziwa kuchereza alendo. Makhalidwe amenewa anamuthandiza kuti akwaniritse bwino udindo wake monga mkazi wokwatiwa, kholo komanso mtumiki wa Mulungu woona.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Rabeka, werengani nkhani yakuti “Inde Ndipita.”

  Rute

 Kodi anali ndani? Anali mkazi wachimoabu amene anasiya milungu ya kwawo n’kupita ku Isiraeli kuti azikalambira Yehova.

 Kodi anachita zotani? Rute anasonyeza kuti ankakonda kwambiri apongozi ake a Naomi. Naomi ndi mwamuna wake komanso ana awo awiri anasamukira ku Mowabu chifukwa cha njala yomwe inali ku Isiraeli. Kenako anawo anakwatira akazi achimowabu, Rute ndi Olipa. Patapita nthawi, mwamuna wake wa Naomi ndi ana ake awiri aja anamwalira n’kusiya akazi atatu onsewa ali amasiye.

 Njala itatha, Naomi anaganiza zobwerera kwawo ku Isiraeli. Rute ndi Olipa ankafuna kupita nawo. Koma Naomi anawauza kuti abwerere kwa achibale awo. Olipa anabwereradi. (Rute 1:1-6, 15) Koma Rute anaumirirabe kukhala ndi apongozi akewo. Iye ankakonda kwambiri Naomi ndipo ankafuna kuti azikalambira Yehova, Mulungu wa Naomi.—Rute 1:16, 17; 2:11.

 Mbiri yoti Rute ndi wokhulupirika komanso wolimbikira ntchito, inafalikira m’tauni ya Betelehemu, kwawo kwa Naomi. Munthu wina wolemera wa ku Betelehemu dzina lake Boazi anachita chidwi kwambiri ndi Rute ndipo ankamupatsa chakudya cha iyeyo ndi Naomi. (Rute 2:5-7, 20) Pamapeto pake Rute anakwatiwa ndi Boazi ndipo anakhala kholo la Mfumu Davide komanso Yesu Khristu.—Mateyu 1:5, 6, 16.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Rute anachita? Rute analolera kuchoka kwawo n’kusiya achibale ake chifukwa chokonda Naomi komanso Yehova. Iye anali wolimbikira ntchito, wodzipereka ndiponso wokhulupirika, ngakhale pamene ankakumana ndi mavuto.

  Sara

 Kodi anali ndani? Anali mkazi wa Abulahamu komanso mayi ake a Isaki.

 Kodi anachita zotani? Sara anasiya moyo wofewa womwe anali nawo mumzinda wotukuka wa Uri chifukwa chokhulupirira zimene Mulungu analonjeza Abulahamu mwamuna wake. Mulungu anauza Abulahamu kuti achoke ku Uri n’kupita ku Kanani. Anamulonjeza kuti amudalitsa komanso kuti adzachulukitsa ana ake kukhala mtundu waukulu. (Genesis 12:1-5) N’kutheka kuti pa nthawiyi Sara anali ndi zaka za m’ma 60. Koma kungochokera nthawi imeneyo, Sara ndi mwamuna wake Abulahamu anayamba moyo womangosamukasamuka, moti ankangokhala m’mahema.

 Ngakhale kuti kuyendayendaku kunachititsa kuti moyo wa Sara ukhale pangozi, Sara ankathandiza Abulahamu pomvera zomwe Mulungu wamuuza. (Genesis 12:10, 15) Sara anakhala wopanda mwana kwa zaka zambiri ndipo zimenezi zinkamukhumudwitsa kwambiri. Komabe Mulungu anali atalonjeza kale kuti adzadalitsa mbewu ya Abulahamu. (Genesis 12:7; 13:15; 15:18; 16:1, 2, 15) Patapita nthawi, Mulungu anatsimikizira Sara kuti adzaberekera Abulahamu mwana. Sara anaberekadi ngakhale kuti pa nthawiyi anali atakalamba ndiponso atadutsa nthawi yoti angabereke. Anali ndi zaka 90 ndipo mwamuna wake anali ndi zaka 100. (Genesis 17:17; 21:2-5) Mwanayo anamupatsa dzina lakuti Isaki.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Sara anachita? Chitsanzo cha Sara chikutiphunzitsa kuti nthawi zonse tizikhulupirira kuti Mulungu akwaniritsa zimene walonjeza ngakhale pa zomwe zikuoneka ngati zosatheka. (Aheberi 11:11) Ndipo zimene anachita monga mkazi wokwatiwa zimasonyeza kufunika kokhala munthu waulemu m’banja.—1 Petulo 3:5, 6.

  •   Kuti mudziwe zambiri zokhudza Sara, werengani nkhani yakuti “Ndiwe Mkazi Wokongola” ndi yakuti “Mulungu Anamutchula Kuti ‘Mfumukazi.’

  Msulami

 Kodi anali ndani? Anali mtsikana wokongola kwambiri wakumudzi ndipo mbali yaikulu m’buku la Nyimbo ya Solomo imafotokoza za iyeyo. Baibulo silimatchula dzina lake lenileni.

 Kodi anachita zotani? Mtsikanayu anakhalabe wokhulupirika kwa wokondedwa wake yemwe anali m’busa wa ziweto. (Nyimbo ya Solomo 2:16) Popeza kuti anali wokongola kwambiri, Mfumu Solomo yomwe inali yolemera inayamba kukopeka naye ndipo anayesetsa kumunyengerera. (Nyimbo ya Solomo 7:6) Ngakhale kuti anthu ena ankamulimbikitsa kuti akwatirane ndi Solomo, mtsikanayu anakana. Iye ankakonda kwambiri m’busa wa ziweto uja yemwe anali wosauka ndipo anali wokhulupirika kwa mnyamatayo.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Msulami anachita? Ngakhale kuti anali wokongola kwambiri komanso panali anthu ambiri amene ankakopeka naye, ankachita zinthu modzichepetsa. Sanalole kusokonezedwa ndi zonena za anthu ena, chuma, kapena kutchuka. Iye anayesetsa kukhala wodziletsa ndipo sanachite chilichonse cholakwika.

  Mkazi wa Loti

 Kodi anali ndani? Baibulo silitchula dzina lake. Koma limanena kuti anali ndi ana awiri aakazi komanso kuti ankakhala ku Sodomu limodzi ndi banja lake.—Genesis 19:1, 15.

 Kodi anachita zotani? Mkazi wa Loti sanamvere lamulo la Mulungu. Mulungu anali atatsimikiza zowononga Sodomu ndi mizinda ina yoyandikana nayo chifukwa cha khalidwe lachiwerewere lomwe linafika poipa kwambiri. Koma popeza kuti Mulungu ankakonda Loti ndi banja lake omwe anali okhulupirika ndipo ankakhala ku Sodomu, anatumiza angelo awiri kuti awaperekeze pothawa mumzindawo.—Genesis 18:20; 19:1, 12, 13.

 Angelowo anauza Loti ndi banja lake kuti athawe m’deralo ndipo asayang’ane m’mbuyo chifukwa angafe. (Genesis 19:17) Koma mkazi wa Loti “anacheukira kumbuyo, ndipo anasanduka chipilala chamchere.”—Genesis 19:26.

 Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene mkazi wa Loti anachita? Nkhani ya mkazi wa Loti imatithandiza kumvetsa kuopsa kokonda kwambiri katundu amene tili naye mpaka kufika polephera kumvera Mulungu. Yesu anagwiritsa ntchito nkhani ya mkazi wa Loti monga chenjezo. Iye anati: “Kumbukirani mkazi wa Loti.”—Luka 17:32.

 Tchati Chosonyeza Akazi Otchulidwa m’Baibulo

  1.  Hava

  2. Chigumula (2370 B.C.E.)

    1.  Sara

    2.  Mkazi wa Loti

    3.  Rabeka

    4.  Leya

    5.  Rakele

  3. Ulendo wa Aisiraeli (1513 B.C.E.)

    1.  Miriamu

    2.  Rahabi

    3.  Rute

    4.  Debora

    5.  Yaeli

    6.  Delila

    7.  Hana

  4. Mfumu yoyamba ya Isiraeli (1117 B.C.E.)

    1.  Abigayeli

    2.  Msulami

    3.  Yezebeli

    4.  Esitere

    5.  Mariya (mayi ake a Yesu)

  5. Ubatizo wa Yesu (29 C.E.)

    1.  Marita

    2.  Mariya (mlongo wake wa Marita ndi Lazaro)

    3.  Mariya Mmagadala

  6. Imfa ya Yesu (mu 33 C.E.)