Ayi. Baibulo limatiuza kuti tizipemphera kwa Mulungu yekha, m’dzina la Yesu. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kwa Mulungu yekha, osati kwa anthu oyera mtima, angelo kapena wina aliyense.
Yesu anauzanso otsatira ake kuti: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yohane 14:6, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Mulungu anapereka udindo kwa Yesu yekha woti azitichonderera kwa iye.—Aheberi 7:25.
Kodi pali vuto ngati nditamapemphera kwa Mulungu komanso kwa anthu oyera mtima?
Mulungu anapatsa anthu ake Malamulo Khumi. M’lamulo lina, iye ananena kuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje.” (Ekisodo 20:5, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Kodi mawu akuti Yehova ndi “Mulungu wansanje” akutanthauza chiyani? Mawu a m’munsi palembali mu Baibulo la Dziko Latsopano amanena kuti iye ndi “Mulungu wosalola aliyense kupikisana naye.” Mulungu amafuna kuti anthu azilambira ndiponso kupemphera kwa iye yekha.—Yesaya 48:11.
Mulungu sasangalala tikamapemphera kwa milungu ina kapena anthu ena, ngakhale kwa anthu oyera mtima kapenanso angelo. Pa nthawi ina, mtumwi Yohane ankafuna kulambira mngelo, koma mngeloyo anamuletsa n’kumuuza kuti: “Usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzawo wa abale ako akukhala nawo umboni wa Yesu; lambira Mulungu.”—Chivumbulutso 19:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.