Kodi Ubatizo N’chiyani?

Kodi Ubatizo N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Ubatizo ndi kuviika munthu m’madzi kenako n’kumuvuula. a N’chifukwa chake Yesu anabatizidwa mumtsinje umene unali ndi madzi ambiri. (Mateyu 3:13, 16) Munthu winanso wa ku Itiyopiya anapempha kuti abatizidwe ataona “madzi ambiri.”​—Machitidwe 8:36-40.

Zimene ubatizo umatanthauza

 Baibulo limayerekezera ubatizo ndi kuika munthu m’manda. (Aroma 6:4; Akolose 2:12) Munthu akabatizidwa m’madzi amakhala ngati wafa ku moyo wake wakale ndipo wayamba moyo watsopano monga Mkhristu amene wadzipereka kwa Mulungu. Mulungu ndi amene anakonza zoti munthu amene wadzipereka kwa iye azibatizidwa. Zimenezi zimathandiza kuti munthuyo asamadziimbenso mlandu pa machimo omwe analapa chifukwa choti akukhulupirira nsembe ya Yesu Khristu. (1 Petulo 3:21) Mpake kuti Yesu anauza ophunzira ake kuti ayenera kubatizidwa.​—Mateyu 28:19, 20.

Kodi ubatizo wa m’madzi umayeretsa machimo onse a munthu?

 Ayi. Baibulo limaphunzitsa kuti machimo a munthu akhoza kuyeretsedwa kudzera m’magazi a Yesu. (Aroma 5:8, 9; 1 Yohane 1:7) Munthu angapindule ndi nsembeyi akamakhulupirira Yesu komanso kusintha moyo wake kuti azichita zimene Yesuyo amaphunzitsa ndiponso kubatizidwa.​—Machitidwe 2:38; 3:19.

Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti makanda azibatizidwa?

 Ayi. Baibulo siliphunzitsa kuti makanda azibatizidwa. Komabe matchalitchi ena amachita mwambo “wobatiza” makanda powawaza kapena kuwadonthezera madzi pamutu kenako amawapatsa mayina. Akhristu oona amabatiza anthu amene amatha kumvetsa zinthu komanso amakhulupirira “uthenga wabwino wonena za ufumu wa Mulungu.” (Machitidwe 8:12) Munthu akamva Mawu a Mulungu amafunika kuwakhulupirira komanso kulapa. Komatu mwana wakhanda sangachite zimenezi.​—Machitidwe 2:22, 38, 41.

 Komanso Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amaona kuti ana aang’ono ndi oyera potengera kukhulupirika kwa makolo awo amene ndi Akhristu. (1 Akorinto 7:14) Zikanakhala kuti Baibulo limalola kubatiza makanda, ndiye kuti panalibe chifukwa chovomerezera kuti anawo azikhala oyera potengera kukhulupirika kwa makolo awo. b

Maganizo olakwika okhudza Ubatizo wa Akhristu

 Maganizo olakwika: Kuwaza kapena kudontheza madzi pamutu pa munthu ndi njira yachidule yobatizira m’malo momuviika m’madzi.

 Zoona zake: Nkhani zonse za m’Baibulo zonena za anthu omwe anabatizidwa zimasonyeza kuti anthuwo ankaviikidwa m’madzi. Mwachitsanzo, pamene Filipo ankabatiza munthu wa ku Itiyopiya “anatsika ndi kulowa m’madzimo” kuti amubatize. Kenako, ‘anatuluka m’madzimo.’​—Machitidwe 8:36-39. c

 Maganizo olakwika: Baibulo limasonyeza kuti pa nthawi imene mabanja ena ankabatizidwa, makandanso anabatizidwa nawo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za munthu wina woyang’anira ndende wa ku Filipi, kuti: “Iye ndi a m’banja lake, anabatizidwa.”​—Machitidwe 16:20-34.

 Zoona zake: Nkhani ya munthu woyang’anira ndendeyu ikusonyeza kuti anthu amene anabatizidwawo anamvetsa “mawu a Yehova” komanso “anakondwera kwambiri.” (Machitidwe 16:32, 34) Zimenezi zikusonyeza kuti makanda amene anali m’nyumba ya woyang’anira ndendeyo sakanabatizidwa chifukwa choti sakanatha kumvetsa bwino mawu a Yehova.

 Maganizo olakwika: Yesu anaphunzitsa za ubatizo wamakanda pamene ananena kuti Ufumu Wakumwamba ndi wa ana aang’ono.​—Mateyu 19:13-15; Maliko 10:13-16.

 Zoona zake: Pa nthawiyi, Yesu sankanena za ubatizo. Koma ankatanthauza kuti anthu amene akufuna kudzalowa mu Ufumu wa Mulungu ayenera kukhala ngati ana aang’ono chifukwa ana amakhala ofatsa komanso savuta kuwaphunzitsa.​—Mateyu 18:4; Luka 18:16, 17.

a Malinga ndi zimene buku lina linanena, mawu Achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “ubatizo” anachokera ku mawu akuti “kuviika.”​—Theological Dictionary of the New Testament, Volume I, page  529.

b Buku lina linanena kuti, “m’Baibulo la Chipangano Chatsopano mulibe lemba losonyeza kuti makanda ayenera kubatizidwa.” Bukuli linanenanso kuti ubatizo wa makanda unachokera pa “maganizo olakwika komanso ongokokomeza omwe anthu anali nawo pa nkhani ya kufunika kwa ubatizo.” (The International Standard Bible Encyclopedia, Volume 1, page 416-​417) Anthuwo anali ndi maganizo akuti ubatizo paokha umachotseratu machimo a munthu.

c Buku lina linanena kuti: “Pali umboni wakuti M’tchalitchi choyambirira, munthu ankamuviika m’madzi pomubatiza.”—New Catholic Encyclopedia, Volume 2, page 59.