Kodi Zipembedzo Zonse N’zofanana Ndipo Zimathandizadi Anthu Kudziwa Mulungu?
Yankho la m’Baibulo
Ayi, zipembedzo zonse sizofanana. M’Baibulo muli zitsanzo za zipembedzo zimene sizisangalatsa Mulungu. Zipembedzozi zilipo magulu awiri.
Gulu loyamba: Zipembedzo zolambira milungu yonyenga
Baibulo limanena kuti kulambira milungu yonyenga ndi ‘kopanda pake,’ ‘kwachabechabe’ ndiponso ‘kosapindulitsa.’ (Yeremiya 10:3-5; 16:19, 20) Yehova a Mulungu analamula mtundu wa Aisiraeli kuti: “Usakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.” (Ekisodo 20:3, 23; 23:24) Pamene Aisiraeli anayamba kulambira milungu yonyenga, “mkwiyo wa Yehova unawayakira.”—Numeri 25:3; Levitiko 20:2; Oweruza 2:13, 14.
Masiku anonso Yehova amakwiya ndi anthu olambira “milungu” yonyenga. (1 Akorinto 8:5, 6; Agalatiya 4:8) Iye amalamula anthu amene akufuna kumulambira kuti ayenera kutuluka m’chipembedzo chonyenga, ndipo amati: “Tulukani pakati pawo, lekanani nawo.” (2 Akorinto 6:14-17) Zikanakhala kuti zipembedzo zonse n’zofanana ndipo zimathandizadi anthu kudziwa Mulungu, ndiye n’chifukwa chiyani Mulungu anapereka lamulo limeneli?
Gulu lachiwiri: Zipembedzo zolambira Mulungu woona m’njira yosavomerezeka
Nthawi zina Aisiraeli ankalambira Mulungu pogwiritsa ntchito zikhulupiriro ndiponso miyambo yochokera kwa anthu amene ankalambira milungu yonyenga. Koma Yehova ankadana ndi zoti anthu aziphatikiza kulambira koona ndi konyenga. (Ekisodo 32:8; Deuteronomo 12:2-4) Yesu anadzudzula atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake chifukwa cha zimene ankachita polambira Mulungu. Iwo ankadzionetsera kuti amalambira Mulungu koma zoona zake n’zakuti anali achinyengo chifukwa ‘ankanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.’—Mateyu 23:23.
Masiku anonso chipembedzo chokhacho chimene chimaphunzitsa zoona n’chimene chingathandize anthu kudziwa Mulungu. Zinthu zoona zokhudza Mulungu zimapezeka m’Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17; 2 Timoteyo 3:16, 17) Zipembedzo zimene zimaphunzitsa zinthu zosemphana ndi zimene zili m’Baibulo sizingathandize anthu mpang’ono pomwe kudziwa Mulungu. Ziphunzitso zambiri zimene anthu amaganiza kuti ndi za m’Baibulo monga zakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi, munthu ali ndi mzimu wosafa ndiponso zoti anthu oipa amakazunzidwa kumoto, zinachokera kwa anthu amene ankalambira milungu yonyenga. Zipembedzo zimene zimaphunzitsa zimenezi n’zosathandiza chifukwa zimaphunzitsa miyambo ya anthu m’malo mophunzitsa zimene Mulungu amafuna.—Maliko 7:7, 8.
Mulungu amadana ndi kumulambira mwachinyengo. (Tito 1:16) Chipembedzo choona chiyenera kuthandiza anthu kukhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu osati chizingokhala ndi miyambo inayake kapenanso kuti anthu azingopemphera mwamwambo chabe. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake. Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo, ndi kukhala wopanda banga la dzikoli.” (Yakobo 1:26, 27) Baibulo la King James Version, limagwiritsa ntchito mawu akuti “chipembedzo chosadetsedwa” ponena za kulambira Mulungu mopanda chinyengo.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS
Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?
Anthu amaganiza kuti palibe vuto ngati munthu atalowa m’chipembedzo chilichonse.
Mfundo Zofunika za M'Baibulo—Mavidiyo
Kodi Mulungu Amafuna Kuti Anthu Azigwiritsa Ntchito Zizindikiro Pomulambira?
Kodi zingatithandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu yemwe sitingamuone?
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA
Yambani kuphunzira Baibulo
Phunzirani Baibulo kwaulere, mochita kukambirana ndi mphunzitsi wanu.
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO