Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda? YAMBANI Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda? Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Yankho la m’Baibulo Inde. Mulungu amaganizira atumiki ake amene akudwala. Ponena za mtumiki wa Mulungu wokhulupirika, Baibulo limati: ‘Yehova adzamuchirikiza pamene akudwala pabedi lake.’ (Salimo 41:3) Ngati mukudwala matenda enaake, mfundo zitatu zotsatirazi zingakuthandizeni kupirira. Muzipempha Mulungu kuti akupatseni mphamvu. Mulungu angakupatseni ‘mtendere wake umene umaposa kuganiza mozama kulikonse,’ womwe ungakuthandizeni kuti mupirire komanso kuti musamade nkhawa kwambiri.—Afilipi 4:6, 7. Muziyesetsa kukhala wosangalala. Baibulo limati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.” (Miyambo 17:22) Muziyesetsa kuseka kapena kuchita tinthabwala chifukwa zimenezi zimathandiza kuti muziiwalako mavuto. Izi zingathandizenso kuti musamavutike kwambiri ndi matendawo. Muzikhulupirira zimene Mulungu walonjeza. Mukamayembekezera zinthu zabwino mukhoza kukhala osangalala ngakhale kuti mukuvutika ndi matenda. (Aroma 12:12) Baibulo limatiuza kuti m’tsogolomu, palibe munthu amene “adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Pa nthawiyo, Mulungu adzathetsa matenda onse, ngakhale amene anthu akulephera kuwachiza masiku ano. Mwachitsanzo, Baibulo limanena zimene Mulungu adzachite pothetsa ukalamba. Limati: “Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.”—Yobu 33:25. Dziwani izi: A Mboni za Yehova amadziwa kuti Mulungu amathandiza anthu amene akudwala koma nawonso amalandira chithandizo chamankhwala akadwala. (Maliko 2:17) Sitilimbikitsa anthu kulandira chithandizo chinachake chifukwa munthu aliyense ayenera kusankha yekha chithandizo chimene akufuna. Nkhani Zina Baibulo Kuvutika Kuyankha Mafunso a M’Baibulo Moyo Wanthanzi Mtendere Komanso Moyo Wosangalala Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika? Anthu ambiri amafuna kudziwa kuti n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri. Baibulo limapereka yankho logwira mtima pa nkhaniyi. ZOKHUDZA IFEYO Pemphani Kuti Tidzakuyendereni Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova. Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda? KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda? Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda? https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/502013105/univ/art/502013105_univ_sqr_xl.jpg