Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti ‘Nthawi ya Mapeto’ N’chiyani?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zidzakhala zizindikiro za “mapeto a nthawi ino,” kapena “mathedwe a nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 24:3; King James Version) Baibulo limati nthawi imeneyi ndi “masiku otsiriza” komanso “nthawi yamapeto.” (2 Timoteyo 3:1; Danieli 8:19; Easy-to-Read Version) Baibulo linalosera zizindikiro za masiku otsiriza ndipo zina mwa zizindikiro zikuluzikulu za masiku otsiriza ndi:
Nkhondo m’mayiko osiyanasiyana.—Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:4.
Njala.—Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:5, 6.
Zivomezi zamphamvu.—Luka 21:11.
Miliri, kapena kubuka kwa “matenda oopsa.”—Luka 21:11, Contemporary English Version.
Kuwonjezereka kwa kuphwanya malamulo.—Mateyu 24:12.
Anthu akuononga kwambiri dziko.—Chivumbulutso 11:18.
Kulowa pansi kwa makhalidwe abwino, monga mmene anthu ambiri akuchitira omwe ndi “osayamika, osakhulupirika, . . . osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada.”—2 Timoteyo 3:1-4.
Kusokonekera kwa mabanja omwe anthu ake ndi “osakonda achibale awo” komanso ana omwe ndi “osamvera makolo.”—2 Timoteyo 3:2, 3.
Kuchuluka kwa anthu osakonda Mulungu.—Mateyu 24:12.
Zochita za chinyengo za zipembedzo.—2 Timoteyo 3:5.
Kuwonjezereka kwa kumvetsa bwino maulosi a m’Baibulo, kuphatikizapo maulosi okhudza masiku otsiriza.—Danieli 12:4.
Ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse.—Mateyu 24:14.
Kuchuluka kwa anthu osafuna kuvomereza komanso onyoza umboni wosonyeza kuti mapeto atsala pang’ono.—Mateyu 24:37-39; 2 Petulo 3:3, 4.
Kukwaniritsidwa kwa maulosi onsewa okhudza masiku otsiriza pa nthawi imodzi, osati ochepa chabe koma ambiri mwa maulosiwo.—Mateyu 24:33.
Kodi tikukhaladi ‘m’masiku otsiriza’?
Inde. Zimene zikuchitika masiku ano komanso zimene Baibulo limafotokoza kuti zinkachitika m’mbuyomu zimasonyeza kuti masiku otsiriza anayamba mu 1914. M’chaka chimenechi, Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kumwamba. Chinthu choyamba chimene Ufumuwu unachita, ndi kuthamangitsa Satana ndi ziwanda kuchoka kumwambako kubwera padziko lapansi ndipo sanaloledwenso kubwerera kumwamba. (Chivumbulutso 12:7-12) Masiku ano Satana wachititsa kuti anthu ambiri akhale ndi makhalidwe komanso maganizo oipa ndipo zimenezi zapangitsa kuti masiku otsiriza akhale “nthawi yapadera komanso yovuta.”—2 Timoteyo 3:1.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
Mfundo Zofunika za M'Baibulo—Mavidiyo
Ufumu wa Mulungu Unayamba Kulamulira mu 1914
Zaka zoposa 2,500 zapitazo, Mulungu anapatsa mfumu yamphamvu loto lonena za ulosi umene ukukwaniritsidwa panopa.
ZOKHUDZA IFEYO
Pemphani Kuti Tidzakuyendereni
Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova.
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO