Kodi Mulungu Amangopezeka Pena Paliponse?
Yankho la m’Baibulo
Mulungu amatha kuona chilichonse komanso kuchita zinthu kwina kulikonse komwe akufuna. (Miyambo 15:3; Aheberi 4:13) Komabe Baibulo siliphunzitsa kuti Mulungu amangopezeka paliponse nthawi ina iliyonse. M’malomwake limasonyeza kuti Mulungu ali ndi malo ake okhala ngati mmene ziliri ndi anthufe.
Mmene Mulungu alili: Mulungu ndi mzimu. (Yohane 4:24) Palibe munthu amene angathe kumuona. (Yohane 1:18) Masomphenya onena za Mulungu omwe ali m’Baibulo nthawi zonse amasonyeza kuti Mulungu ali ndi malo ake enieni amene amakhala. Baibulo silinena kuti amangopezeka pena paliponse.—Yesaya 6:1, 2; Chivumbulutso 4:2, 3, 8.
Kumene Mulungu amakhala: Mulungu amakhala malo amene kuli zolengedwa zauzimu ndipo malowa ndi osiyana kwambiri ndi malo okhala anthu ndi nyama. Mulungu ali ndi malo ake “okhala, kumwamba” komwe kuli zolengedwa zauzimu. (1 Mafumu 8:30) Baibulo limanena kuti pa nthawi ina zolengedwa zauzimu zinapita “kukaonekera pamaso pa Yehova.” a Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu ali ndi malo ake enieni amene amakhalako.—Yobu 1:6.
Ngati Mulungu samangopezeka pena paliponse, kodi angandisamaliredi ineyo pandekha?
Inde. Mulungu amasamalira munthu wina aliyense payekha. Ngakhale kuti amakhala kumwamba komwe ndi kwa zolengedwa zauzimu, Mulungu amachita chidwi ndi anthu omwe ali padziko amene amachita zinthu zomusangalatsa ndipo amawasamalira. (1 Mafumu 8:39; 2 Mbiri 16:9) Taonani mmene Yehova amasonyezera kuti amadera nkhawa anthu amene amamulambira ndi mtima wonse:
Pamene mukupemphera: Yehova amatha kumva pemphero lanu pa nthawi imene mukupempherayo.—2 Mbiri 18:31.
Pamene mwasokonezeka maganizo: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Salimo 34:18.
Pamene mukufunika malangizo: Yehova anati: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.” Iye amachita zimenezi pogwiritsa ntchito Mawu ake Baibulo.—Salimo 32:8.
Maganizo olakwika okhudza zinthu zomwe zimapezeka pena paliponse
Maganizo olakwika: Mulungu amapezeka pena paliponse m’chilengedwechi.
Zoona zake: Mulungu sakhala padziko lapansi kapena pena paliponse m’chilengedwe chomwe timatha kuchiona ndi maso. (1 Mafumu 8:27) N’zoona kuti nyenyezi komanso zinthu zina za m’chilengedwe ‘zimalengeza ulemerero wa Mulungu.’ (Salimo 19:1) Munthu amene wajambula chithunzi china chake, sakhala m’chithunzi chimene wajambulacho. Komabe, chithunzicho chimatiuza zina zake zokhudza wojambulayo. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu nayenso sakhala m’zinthu zimene analenga. Koma ngakhale zili choncho, chilengedwe chimatiuza ‘makhalidwe osaoneka’ a Mlengi monga mphamvu zake, nzeru komanso chikondi chake.—Aroma 1:20.
Maganizo olakwika: Mulungu ayenera kumapezeka pena paliponse kuti azidziwa zinthu zonse komanso kuti akhale wamphamvuyonse.
Zoona zake: Mzimu woyera wa Mulungu, ndi mphamvu imene iye amagwiritsa ntchito. Pogwiritsa ntchito mzimu wake, Mulungu angathe kuzindikira kapena kuchita china chilichonse, kwina kulikonse komanso pa nthawi iliyonse, popanda iyeyo kukhala kumaloko.—Salimo 139:7.
Maganizo olakwika: Lemba la Salimo 139:8 limanena kuti Mulungu amapezeka pena paliponse chifukwa limati: “Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko. Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko.”
Zoona zake: Lembali silikunena za malo amene Mulungu amapezeka. Koma m’malomwake, likungosonyeza kuti Mulungu sangalephere kutichitira zina zake chifukwa cha malo amene tili.
a Yehova ndi dzina la Mulungu limene limapezeka m’Baibulo.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?
Pali zifukwa zomveka zimene Baibulo limatchulira mzimu woyera kuti ndi “manja” a Mulungu.
ZOKHUDZA IFEYO
Pemphani Kuti Tidzakuyendereni
Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova.
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO