Mavidiyo Othandiza Kumvetsa Mfundo Zofunika za M’baibulo

Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?

Mulungu ali ndi maina ambiri audindo monga akuti Atate, Mlengi ndi Ambuye. Koma Dzina lake lenileni limapezeka m’Baibulo malo oposa 7000.

Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani?

Ngati Baibulo linalembedwa ndi anthu, kodi n’zomveka kunena kuti ndi Mawu a Mulungu? Kodi m’Baibulo muli mawu a ndani?

Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

Ngati Baibulo linachokeradi kwa Mulungu, ndiye kuti liyenera kukhala losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?

Padziko lapansili pali zinthu zambiri zokongola. Mulungu anaika dzikoli pamalo abwino kwambiri kuchokera pamene pali dzuwa ndipo limazungulira pa liwiro labwino. N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansili mwanjira imeneyi?

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

Baibulo limanena kuti kutsogoloku anthu ambiri adzaukitsidwa ngati mmene zinakhalira ndi Lazaro.

N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?

Baibulo limasonyeza kuti imfa ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Kodi imfa ya Yesu ili ndi phindu lililonse?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Ali padziko lapansi, Yesu anafotokoza kwambiri za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Kwa zaka zambiri otsatira ake akhala akupempherera Ufumu umenewu kuti ubwere.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

Anthu ambiri amafuna kudziwa kuti n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri. Baibulo limapereka yankho logwira mtima pa nkhaniyi.

Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?

Anthu amaganiza kuti palibe vuto ngati munthu atalowa m’chipembedzo chilichonse.

Kodi Mulungu Amamvetsera Mapemphero Onse?

Nanga bwanji ngati munthu akupempha zinthu zinazake chifukwa cha dyera? Bwanji ngati mwamuna atamenya mkazi wake, kenako n’kumapempha Mulungu kuti amudalitse?